Chichewa

Chonona chifumira kudzira

Listen to this article

 

Tikamakamba za kufunika kuti pasamakhale kusiyana pa mwayi womwe amayi ndi abambo akupatsidwa, titamakumbuka za mwambi uwu wakuti chonona chifumira kudzira.

Izitu zikutanthauza kuti kusintha kwenikweni pakhalidwe la anthu kwagona pa momwe anthu akuleredwera m’makomo mwawo, m’madera momwe tikukhala, m’mipingo komanso kusukulu. Chimodzimodzinso nkhani ya kuthetsa nkhanza m’mabanja komanso nkhanza zina zomwe anthu amakumana nazo kaamba koti ndi aakazi kapena aamuna, tikumbuke ndithu kuti nthawi youmba khalidwe la munthu ndi nthawi yomwe akukula.

Mwachitsanzo, anthu ambiri-abambo ngakhalenso amayi-amene amakhala ndi mtima woderera amayi, amakhala kuti adakula pakati pa chikhalidwe chomwe chimaonera amayi pansi. Anthu oterewa amavuta kuti akhale pansi pautsogoleri wa mzimayi chifukwa amangoona kuti munthu amene akuwalamula sakuyenera kutero.

Chikhalidwe cholakwikachi chimakhala chokhazikika m’mitu mwawo ndipo kukonza kwake akakula kumakhala kovuta. Tsono udindo wambiri wokonza makhalidwe olakwikawa uli m’manja mwa makolo poonetsetsa kuti nzika zomwe mukulera zikhale ndi zikhulupiriro komanso makhalidwe oyenerera osapondereza, kuzunza kapena kuderera anthu ena kaamba ka momwe adabadwira.

Amayi amene azunzika m’mabanja ndipo ali ndi ana aamuna, akhoza kuonetsetsa kuti mwana amene akulera uja asadzakhale ngati bambo ake kuti adzazunzenso mkazi wake akakula. Ana aamuna aphuzitsidwe kulemekeza munthu wamayi. Adziwe kuti kusiyana kwawo ndi munthu wamkazi kwagona pa kaumbidwe ka ziwalo zawo pakabadwidwe.

Zikakhala nzeru ndi machitachita ena palibe kusiyana. Auzidwe ana aamuna kuti mzimayi ndi muthu ngati iwo. Si chida chongoti wina akafuna agone nacho kapena kumamunyozetsa kumamuimbira miluzi akamayenda m’misewumu.

Chimodzimodzinso ana akazi tiwaphunzitse kuti ali ndi kuthekera kofikira komanso kukhala chilichonse chomwe angafune pamoyo wawo. Tiwaphunzitse atsikana kuti asadalire thumba la munthu wammuna chifukwa chomwe bambo akuchita kuti apeze ndalama pakhomo iwonso akhoza kupanga.

Mtsikana asalunjike nzeru zake pa thupi lake. Pali luso, nzeru ndi zinthu zina zomwe anadalitsidwa nazo kuti zipindulire iye komanso dziko.

Aphunzitsidwenso mwana wamkazi kuti asalole munthu aliyense kumukokera pansi kapena kumuchitira nkhanza-angakhale mbale kaya mwamuna wake. Mwanayo auzidwe akali wamng’ono kukana ndi kusapirira mtundu uliwonse wa nkhanza.

Pali zitsanzo zambiri zomwe tikhoza kuphunzirirapo n’kuona kuti ana amene tikulera tiwaongola bwanji kuti mawa lino asachitidwe nkhanza komanso asakhale zida zopsinjira ena n’kumapititsa patsogolo moyo wankhanza. Pozindikira kuti mwana saleredwa pakhomo pa makolo ake okha, sukulu, mipingo ndi madera mukufunika kuunikira n’kupeza njira zoongolera ana kuti asakule mopotoka. n

Related Articles

Back to top button
Translate »