Chichewa

Chotsani chiletso chogulitsa chimanga kunja—MCCCI

Listen to this article

 

Bungwe loona za malonda ndi mafakitale la Malawi Confederation of Chambers of Commerce and Industry (MCCCI) lapempha boma kuti lichotse chiletso chogulitsa chimanga kunja.

Pulezidenti wa bungwelo Karl Chokotho adapereka pempholi Lachinayi potsegulira chionetsero cha malonda ku Gateway Mall mumzinda wa Lilongwe.

Iye adati chiletsochi chikupsinja kwambiri alimi ang’onoang’ono chifukwa omwe akukakamizidwa kugulitsa chimanga chawo m’dziko mom’muno pa mitengo yotsika poyerekeza ndi mitengo yomwe maiko ena akugulira.

Chokotho: Alimi
akadapha makwacha

“Pa Tanzania pomwepa, chimanga chikugulidwa pamtengo okwera mwina kuposa katatu mtengo wa boma la Malawi ndiye alimi akadaloledwa kuti azigulitsa chimanga chawo m’misika ngati imeneyi, akadapha makwacha,” adatero Chokotho.

Iye adati akudziwa kuti dziko la Malawi likuyenera kugula ndi kusunga chimanga kupangira zogwa chaka cha mawa zomwe sizikudziwika koma adati vuto lomwe lilipo ndi loti bungwe la Admarc lomwe limagulako bwino silikugulanso chimangachi.

“Boma litakhazikitsa mitengo, alimi adali ndi chiyembekezo kuti mwina apindula pogulitsa ku Admarc koma n’zosabisa kuti Admarc siyikugula chimanga moti alimi akungobwerera nacho mapeto ake mavenda akupezerapo danga,” adatero Chokotho.

Nduna ya za ntchito, achinyamata, masewero ndi kuphunzitsa anthu ntchito, Francis Kasaila, yemwe adali mlendo wolemekezeka pa mwambowo, adati mpofunika kuzama ndi kukambirana bwinobwino chiletsochi chisadachotsedwe.

Ndunayo idati alimi ambiri ang’onoang’ono amadalira pologalamu ya boma ya sabuside paulimi pomwe omwe amagulitsa chimanga kunja ndi mavenda zomwe zikutanthauza kuti kuchotsa chiletsochi ndiye kuti mavenda ndiwo apindule pa sabuside ya boma.

“Vuto lalikulu ndi loti omwe amagulitsa chimanga kunja ndi mavenda omwe amagula kwa alimi pamitengo yolira ndiye zikutanthauza kuti olo titachotsa chiletsochi, alimiwo sathandizika ayi agulidwabe pa mtengo olirawo ndipo mavenda ndiwo apindule,” adatero Kasaila.

Iye adati ngati abizinesi akufuna kumachita malonda achimanga kunja, akuyenera kulowerera pa ulimi wamthirira kuti azigulitsa zomwe alima okha. n

Related Articles

Back to top button
Translate »