Chichewa

Chu uyu mpaka liti?

Listen to this article

 

Njala yayamba kuluma m’madera ena koma ngakhale zili chonchi, boma lati anthu asayembekezere kuti misika ya Admarc itsegulidwa msanga kaamba koti ntchito yogula chimanga ikadali mkati.

Nduna ya zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi George Chaponda idauza nyuzipepala ya The Nation posachedwapa kuti boma silingatsegule misika lisadamalize kugula poopa kuti mavenda angagule chimanga ku Admarc n’kukagulitsanso ku Admarc komweko.

“Kuti titsegule msika pomwe tikugula, anthu adzagula nkutigulitsanso chifukwa Admarc imagulitsa pamtengo otsika. Zinthu zikalongosoka, tidzalengeza za tsiku lotsegulira msika wa Admarc,” adatero Chaponda.

Gondwe: Mtima pansi
Gondwe: Mtima pansi

Pakalipano, anthu ambiri, makamaka m’boma la Nsanje kuchigwa cha Shire komwe njala yafika kale povuta, akupulumukira mbatata ndi zomera mumtsinje wa Shire zotchedwa nyika zomwe m’miyezi ikudzayi ziyambe kusowa malingana nkuti mbewu ngati izi zimapezeka panyengo yochepa.

Koma njalayi sikuti yakhudza madera akumidzi okha ayi, koma ngakhale m’matauni ndi mizinda ina m’dziko muno.

Maria Kalowekamo, yemwe ndi kholo la ana anayi koma mwamuna wake adamwalira ndipo akukhala kwa Chinsapo mumzinda wa Lilongwe, adati nkhawa yake ili pakuti mbewu ngati mbatata zikayamba kusowa adzavutika kwambiri kusamalira ana akewo.

“Panopa zikuoneka ngati zopepukirako pang’ono chifukwa zakudya zina monga mbatata zikadapezeka m’misikamu koma zikangoyamba kusowa, kukhala mavuto adzaoneni. Boma likadapanga zoti zinthu zisadafike poterepa, chimanga chifikiretu m’misika ya Admarc,” adatero Kalowekamo.

Chisomo Mwale wa ku area 25 mumzinda womwewu, adati polingalira nyimbo ya nthawi zonse ya manyamulidwe a chimanga popita m’misika ya Admarc, bungwe la Admarc

likuyenera kupangiratu ndondomeko zoyenera.

“Vuto lalikulu lomwe limakhalako n’kulephera kukonzekera mokwanira. Mwachitsanzo, misika ya Admarc ikayamba kugulitsa chimanga kumakhala nkhani zosakhala bwino monga za chinyengo, nkhanza ndi mavuto a zamayendedwe. Ino ndiye nyengo yabwino yokonza zinthu ngati zimenezi,” adatero Mwale.

Pa za tsiku lotsegula misika ya Admarc ndi kukonzekera kuthana ndi mavuto omwe anthu akuti amakumana nawo pokagula chimanga, mneneri wa bungwe la Admarc Agnes Chikoko adangoti titsate zomwe idanena nduna.

Koma nduna ya zachuma Goodall Gondwe adati anthu asade nkhawa kwambiri pankhani yopeza chimanga chifukwa boma lakhazikitsa ndalama zokwana K13.2 biliyoni zoti zithandize anthu ovutika kupeza ndalama zogulira chimanga kudzera mupologalamu yogwira ntchito zachitukuko ndi yothandiza anthu okalamba ndi ovutikitsitsa.

“Mavuto onsewo tidawawerengera kale moti panopa tawonjezera thumba la ndalama zomwe anthu amalandira akagwira ntchito zachitukuko za Public Works Programme komanso zomwe timapatsa anthu ovutika kwambiri podzera mupologalamu ya Social Cash Transfer,” adatero Gondwe.

Iye adati K11 biliyoni ndi ya pologalamu ya ntchito zachitukuko pomwe K2.2 biliyoni ndi yogawira anthu ovutikitsitsa mupologalamu ya Social Cash Transfer yomwe cholinga chake chenicheni nkuthandiza anthu kugula chimanga.

Mwa anthu 6.5 miliyoni omwe akhudzidwe ndi njala  chaka chino, anthu 3.9 miliyoni akuyembekezeka kupulumukira pologalamu ya Public Works ndi Social Cash Transfer. n

Related Articles

Back to top button