Clement Banda: Amasirira Aki ndi Popo

Listen to this article

Ndikudziwe bwanawe…

Dzina langa ndine Clement Banda ndipo ndimakhala mumzinda wa Lilongwe ku Area 36.

 

Tandiuze, kodi iwe uli ndi zaka zingati?

Hahahaa, ineyo ndili ndi zaka 27. Bwanji? Mwafunsiranji funso limeneli, amwene?

 

Ndikukuonekerani kuchepa m’maso.

Ayi, ndithu ndidabadwa pakanthawi.

 

Ndimakuona kwambiri m’malo azochitika ukuvina, zimakhala bwanji?

Imeneyo ndiye ntchito yanga moti kupita muzinkhoswe, m’maphwando, misonkhano yosiyanasiyana mudzandipezadi ndikuvina chifukwa anthu ambiri adandizolowera tsopano moti ena ndimachita kukana kuti ndachulukidwa.

 

Udayamba bwanji?

Kuvinaku ndidayamba kalekale. Ndili wamng’ono ndinkakonda kupita kuzochitika za achinyakata zija amati Teen Time moti ndakhalapo katswiri wovina kangapo m’mipikisano imene ija.

 

Ndiye kuti ufike pano?

Zidayamba nthawi imene kudali a Zembani Band ku Golf Club ku Lilongwe pomwe adapereka mwayi woti anthu angapo apite kutsogolo kuti akapikisane kuvina. Ndidapita nawo mpaka mkulu wina wake adandipatsa wotchi ya pamkono chifukwa chondiyamikira.

 

Kenako?

Ndidajoina bandi. Timathandizana kayendetsedwe ka bandiyi ndi anzanga koma ine mbali yanga yeniyeni ndi kukopa anthu tikakhala kuti tikukayimba kwina kwake chifukwa anthu amasangalala zedi ndi kamavina moti ena amanditcha kuti Ankolo Kafula.

 

Iwe umasangalala nazo zimenezi?

Ndilekelenji poti ndimo ndimapezera thandizo langa? Ndipo ndikapanda kumva anthu akutero ndimaona ngati tsiku limenelo ndalephera kusangalatsa mabwana anga omwe ali anthu owonerera.

 

Mbali ya sukulu udafika nayo pati?

Sukulu ndidasiyira Fomu 4.

 

Ndiye kusankha kuvina kusiya sukulu?

Anthu ena akhoza kumaona ngati zamasewera chabe koma ndikupindula kudzera m’njira yomweyi ya kavinidwe kanga komwe ena amati Kafula style koma sikuti ndimangoti basi ndafikapo

Kukadakhala kuti kwathu kuno nkhani ya mafilimu tili nayo chidwi bwenzi ndikadakonda kukhala mmodzi mwa ochita nawo mafilimuwo chifukwa ndimasirira anyamata aja a ku Nigeria afupiafupi ngati ine ndemwe, Aki ndi Popo, koma pano ndi zikhwaya. n

 

Related Articles

Back to top button