Nkhani

Covid-19 yakolera

Listen to this article

Chiwerengero cha Amalawi amene apezeka ndi kachirombo ka coronavirus chatumphuka m’sabata ikuthayi kuchoka pa 101 kufika pa 203.

Izi zachitika pamene komiti yoona za matenda a Covid-19 Lachinayi idalengeza kuti adapeza anthu 102 amene adachokera ku Zimbabwe ndi South Africa adapezeka ndi matendawa.

Ena mwa omwe adafika ku Kamuzu Stadium

Amalawi 441 amene adafika m’dziko muno kuchoka m’dziko la South Africa, m’sabatayi adathawa kumalo amene amawasunga ku Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre. Ndipo dzikoli limyembekeza kulandiranso anthu ena pafupifupi 300 kuchokera ku South Africa dzulo.

Msonkhano wapadera wa komiti ya Covid-19 omwe udali ku Bingu International Convention Centre mumzinda wa Lilongwe Lachinayi, udakambirana mwakuya nkhani zina ndi zina za matendawa koma adagwirizana kuti kuthawa kwa anthu ku Kamuzu Stadium kudachitika kaamba ka kunyozera.

Chiwerengero chambiri cha anthu omwe adapezeka ndi coronavirus m’dziko muno mwezi umodzi wapitawu amakhala anthu omwe adangofika kumene kuchoka m’mayiko okhudzidwa kwambiri ngati Tanzania ndi South Africa.

Koma unduna wa zaumoyo wati kubwera kwa abalewa kusabweretse nkhawa iliyonse chifukwa boma lapanga kale zoyenera kuti anthuwo apimidwe n’kutsimikizika kuti ali bwino asadabwerere m’nyumba zawo.

Mneneri waundunawu Joshua Malango wati ngakhale boma likupanga zotheka kuti kubwera kwa anthuwo kusasokoneze nkhondo yolimbana ndi coronavirus, anthu nawo ali ndi udindo waukulu.

“Takhala tikunena kuti asilikali amphamvu pa nkhondoyi ndi anthu eni ake. Anthu akuyenera kutsatira zomwe amauzidwa kupanga kuti apewe matendawo basi,” adatero Malango.

Mmodzi mwa anthu obwererawo amene sanafune kutchulidwa wadandaula kuti boma silikuonetsa chidwi pa anthuwo chifukwa likuwasunga pamtetete kubwalo la masewero la Kamuzu Stadium ku Blantyre.

“Chifikireni tikungokhala kuno akuti tidikire zotsatira za zomwe adatiyeza ngati tabwera n’kachilomboko kapena ayi koma tikukhala pamtetete,” adatero odandaulayo.

Apo n’kuti anthuwo asanathawe.

Polankhula kwa atolankhani Lachinayi, wapampando wa komiti yapadera ya Covid-19 Dr John Phuka adati kuthawa kwa anthuwo, komwe kudachitika anthu enanso atathawa malo osungirako anthu kwa Kameza mumzinda wa Blantyre, ndi phunziro.

“Takhazikitsa komiti yapadera imene iziunikira momwe anthu ofika kuchoka kunja tikuwalandirira ndi cholinga choti mavuto awa asaonekenso. Ndipepese kwa onse ochoka kunja amene akuoneka kuti anatopa ndi ulendo wochoka ku Joni komanso zochitika,” adatero Phuka.

Koma Malango wati boma lakonza kale malo omwe anthuwo akasungidweko ndipo likhala likulengeza za malo oterowo komanso kusamutsa anthuwo kupita nawo m’malowo.

“Boma likamapanga zinthu limakhala litakonza kale mapulani. Zonsezo zili kale m’mapulani aboma,” adatero Malango.

Woyendetsa ntchito za zaumoyo Dr Charles Mwansambo adati bwalo la Kamuzu Stadium lidasankhidwa ngati pofikira chabe potsata mpata woti anthuwo asathinane malo amodzi mpaka atatengedwera kumalo okhazikika.

Dziko la Malawi lidazemba mbindikiro wa m’nyumba wa masiku 21 kuyambira pa 18 April 2020 mpaka pa 9 May 2020 gulu la zaufulu wa anthu la HRDC litakatenga chiletso polingalira kuti anthu ambiri adalibe chakudya cha panthawi yonse ya mbindikirowo.

M’maiko ena omwe m’bindikirowo udatheka, boma limathandiza anthu ake ndi chakudya komanso ndalama zogulira zinthu zogwiritsa ntchito pa m’bindikirowo.

Related Articles

Back to top button