Chichewa

Dansi ndi Platinum Selector

Listen to this article

 

Kuphunzira ndi chinthu chokoma ndipo ukasakaniza ndi luso lina la manja kukomako kumankira patali. Achinyamata ambiri omwe akuchita bwino ndi kutchuka masiku ano amadalira ntchito zamanja ngakhale sukulu adapita nayo patali. Mmodzi mwa achinyamata oterewa ndi Christopher Nhlane yemwe amadziwika ndi dzina lakuti Platinum Selector yemwe amamveka pa wailesi ya MIJ. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye pa zomwe iye amachita ku wayilesiyi

Tidziwane wawa.

Ndine mwana wa nambala 5 m’banja la ana 7 anyamata atatu ndipo asungwana anayi. Ndimachokera m’bomala Mzimba koma makolo anga amakhala ku Mzuzu. Ndili ndi digiri ya Business Communication yomwe ndidatengera kusukulu ya ukachenjede ya Polytechnic.

Nhlane: Zidayambira kusukulu
Nhlane: Zidayambira kusukulu

Padakalipano umachita chiyani?

Ndimagwira ntchito ku wailesi ya MIJ ngati mtolankhani, muulutsi, mkonzi ndipo nthawi zina ndimapanga mapulogalamu apadera a nyimbo chifukwa kusakaniza nyimbo ndi limodzi mwa maluso omwe ndili nawo.

 

Anthu amakutcha Platinum Selector chifukwa chiyani?

Dzina limeneli ndidaliyambitsa ndekha kalekale mu 2010 nditayamba kuulutsa pulogalamu ya ‘Reggae Uptown’ pawailesi ya MIJ FM. Ndidasankha dzinali polingalira kuti Platinum ndi chitsulo chofewa koma chopirira dzimbiri ndiye inenso pulogalamu yanga siyifwifwa ayi ndimayesetsa kuti ngakhale nyimbo zitakhala zakale koma zimamveka ngati zaimbidwa kumene kutanthauza kuti dzimbiri palibe.

 

Udayamba liti ndipo udayamba bwanji?

Ndidayamba m’chaka cha 2003 ndili pasukulu ya sekondale ya Phwezi. Nthawi imeneyo ndidali ndi chidwi kwambiri ndi akatswiri osakaniza nyimbo monga DJ Banton yemwe panthawiyo ankagwira ntchito ku wailesi ya FM 101.

 

Ankakuthandiza ndani?

Zonse ndinkapanga ndekha ndikafatsa. Ndidali ndi kompyuta yomwe ndidalowetsamo pulogalamu yosakanizira nyimbo ndipo ndimati ndikafatsa ndimakhalira kuyeserera kusakaniza nyimbo mpaka ndidayamba kudzimva kuti tsiku lina ndidzakhala dolo.

 

Munthu yemwe ukakhala sufuna kumuiwala pa luso lako ndi ndani?

Munthu ameneyo ndi Phil Touch yemwe ankandilimbikitsa tikugwira ntchito limodzi ku wayilesi ya MIJ. Adali munthu mmodzi yemwe adasonyeza kuti adali ndi mtima oti ine ndidzakhale dolo osalingalira zoti kaya ndidzamuposa kapena ayi, iye kwake kudali kuwonetsetsa kuti ine ndidziwe basi.

 

Iweyo wagwirako ntchito mmalo ati?

Ndidagwirako ku Malawi News Agency (Mana) kuyambira m’chaka cha 2006 mpaka 2007 kenako m’chaka cha 2010 ndidalowa ntchito ku MIJ komwe ndili mpaka pano.

 

Kupatula kuntchito lusoli umakachitiranso kuti?

Related Articles

Back to top button
Translate »