Chichewa

Dizilo Petulo Palibe, polisi

Listen to this article

 

Nthawi imeneyo nkuti tikudikira Moya Pete kuti atiuze njala athana nayo bwanji pano pa Wenela.

Tonse tidaungana poawailesi kuti timve kuti izi zomagona kumsika wa chimanga nkungololedwa kugula makilogalamu 10 okha zitha liti. Pajatu Dizilo Petulo Palibe mogwirizana ndi Moya Pete adatiuziratu kuti iwo ndi akadaulo pothana ndi njala.

tadeyo

Aliyensetu amadziwa kuti awa ndi akatakwe pothana ndi njala.

Chodabwitsa, 1 koloko yomwe amati atilankhulayo idakwana nkudutsa. 2 koloko idakwana nkudutsa, kuli ziii!

Abiti Patuma adamuimbira mnyamata wodziwa kuika phanzi mkamwa mwake, Geri Waola.

“Kodi zikukhala bwanji? Kumphikako 1 koloko imakwana cha m’ma 4? Tikudikira kumva Moya Pete ife,” adatero Abiti Patuma.

Waola adamuyankha kuti adati 1 koloko idali nthawi yakuti atape mawu a Moya Pete.

Usiku watsikulo, Moya Pete adatipeza pa Wenela.

“Ndithu ndawalambwaza asilikali kuti azigwira akuba chimanga,” adayamba.

“Mukuchita kuwauza chochita? Simesa ndi ntchito yawo? Timayesatu mutiuza kuti mwatipezera chimanga uku ndi uko kuti kung’wemphaku kukhoza kutha,” adatero Abiti Patuma.

Sadayankhe Moya Pete.

“Nanga zinakhala bwanji? Ndimayesa anati mutilankhula tonse 1 koloko?” adaponya funso lina.

“Sanamvetse ndi waola ndi anzake. Ine ndinawauza kuti ayambe kundijambula 1 koloko koma iwo anafalitsa kuti ndinawauza kuti ndikulankhulani nonse okhala pa Wenela nthawi imeneyo. Kaya nkuwatani anthu amenewa kaya,” adatero Moya Pete.

Abiti Patuma adalandira foni. Adalankhula pang’ono nkudula.

Kenako adati: “Tade, tiyeko ku Machinjiri. Mkulu wina akundikodola,” adatero.

Tidalowera komweko. Koma moto umene tidaupeza uko! Kudali kuotcha khoti! Kuotcha bwalo la milandu.

“Anthu akuotchawa si mbanda zimenezi zikufuna milandu yawo isokonekere?” ndidafunsa.

“Kaya. Komai ne ndikuonanso ngati ndi anthu a njala awa. Kutopa akungofuna kupeza pophwetsera,” adandiyankha Abiti Patuma.

Posakhalitsa, chidafika chimbaula. Chidaponya utsi wokhetsa msozi. Pafupi ndi khotilo pali chipatala chaching’ono, kumenenso amayi oyembekezera amachilira.

Ndidaona mayi wina wooneka wotopa akutuluka kuthawa m’chipatalamo. Mayi winanso amene akuoneka kuti adali atangobereka kumene adatulukanso m’chipatalamo, khanda lake lili kumanja. Misozi ili kamukamu. Kakhandako kakungolira.

Utsi wokhetsa msozi. Kodi amenewonso amagula chimanga mozemba pa ka Admarc kopanda kanthu kayandikana ndi khotilo?

Sipadatenge nthawi, tidamva kuti mayi woyembekezera uja adathamangira nyumba ina ndipo chifukwa cha mantha adabereka mwana ngakhale nthawi yake idali isadakwane.

Nthawi yonseyo nkuti apolisiwo atakhamukira malo otsikira basi. Adali kukwapula aliyense.

“Mwaotcha khoti, tiotchanso kamsika kanuka! Mwaiputa dala dungulinya,” adatero mmodzi mwa alonda a bomawo, uku akukwapula mayi wina amene adatsika minibasi.

“Tiyeni tsikani minibasiyo. Mukangotsika muzithawa. Mwagenda kupolisi muli ndi chamba m’thumba!” adatero wapolisi wina.

“Abale kodi anthuwa ndimayesa timawalipira ndife kuti azititeteza? Onani lero akutikwapulanso popanda chifukwa. Bwanji osafufuza amene aotcha khotilo?” adatero Abiti Patuma.

Dizilo Petulo Palibe… Njala… Mizere… Alonda a boma… Nkhanza… Ziwawa ndi zipolowe!!!

Gwira bango iwe, upita ndi madzi! n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »