ChichewaEditors Pick

Dovu lakula ku nsanje

Listen to this article

 

Anthu ena m’boma la Nsanje alephera kupirira nkhuli ndipo akuphabe ndi kugulitsa nyama ya ng’ombe, mbuzi, nkhumba ndi nkhosa mozemba motsutsana ndi chiletso chomwe unduna wa zamalimidwe udakhazikitsa pofuna kuthana ndi matenda a zilonda za m’mapazi ndi mkamwa (foot and mouth disease) omwe adabuka m’bomalo miyezi itatu yapitayo.

Unduna wa zamalimidwe udaletsa kupha kapena kugulitsa ziwetozi m’bomali pa 8 January malinga ndi kubuka kwa matendawo, koma ngakhale chiletsochi sichidachotsedwe, anthu ena akuphabe ng’ombe ndi ziweto zina ndi kugulitsa nyama mozemba, zomwe zikupereka chiopsezo kuti matendawo atha kukhodzokera maboma ena.

Senior Chief Malemia wa m’bomali watsimikiza kuti izi zikuchitikadi ndipo wauza achitetezo m’midzi kuti agwire aliyense amene amupeze akuchita izi.

Malire a Nsanje ndi Chikwawa amayenera kuponda mankhwala
Malire a Nsanje ndi Chikwawa amayenera kuponda mankhwala

“Vuto lake anthuwa akumapha ziweto mozemba, ndiye zikuvuta kuti tiwagwira bwanji, komabe tikuwafufuza ndipo tikawapeza tiwagwira,” adatero Malemia.

Pocheza ndi Msangulutso palamya posachedwapa, Ernest Msambo wa ku Fatima kwa T/A Mlolo m’bomalo adavomereza kuti kumeneko anthu akupha ziweto ndi kugulitsa nyama yake motsutsana ndi chiletso cha boma.

“Achimwene, lija n’kale adaletsa kuti anthu azipha ndi kugulitsa nyama, nkhuli yavuta, komanso anthu a kuno timadalira kupha kapena kugulitsa ziweto kuti tipeze ndalama, n’chifukwa chake anthu akuchita izi mwakabisira. Pamsika nyama sungaipeze, koma mupeza m’makomo anthu akudya nyama,” adatero Msambo.

Koma yemwe akulondoloza momwe nthendayi ikuyendera, Dr. Patrick Chikungwa, adati uku nkulakwa ndipo ngati anthuwa samvera lamulo la boma matendawa atha kufalikira dziko lonse.

“Panopa tili mkati mothana ndi matendawa, ndiye ngati ena akuchita zithu mosemphama ndi ndondomeko yomwe takhazikitsa, asokoneza zomwe tikuchita. Adziwe kuti matendawa angathe kufalikira dziko lonse ngati anthu akuzembetsa ziweto kapena nyama pogwiritsa njira zamadulira,” adatero Chikungwa.

Maboma ena monga Blantyre, Zomba, Mwanza, Mulanje ndi Thyolo kuchigawo cha kummwera amadalira nyama yochokera m’boma la Nsanje ndi Chikwawa.

Malire a bomali ndi Chikwawa pa Sorjin komanso pa Phokera ndi Mtayamoyo paikidwa zipata za mankhwala a madzi omwe munthu aliyense ngakhale galimoto ikamatuluka m’boma la Nsanje, akumapondapo kuti asalowetse matenda m’madera ena.

Koma Chikungwa wati izi sizingathandize kwenikweni ngati ena akudzerabe njira zina osadzera pazipatazi.

“Apapa ndiye kuti angathe kulowetsa nyama m’maboma ena podutsa njira zachidule. Ikalowa m’madera ena ndiye kuti nakonso kufika matendawa ndiye kuthana nawo kwake kudzakhala kovuta kwambiri,” adatero Chikungwa.

Iye adati kufika lero, achita katemera katatu m’bomalo ndipo akudikira kuti aonetsetse ngati nthendayi yatheratu asadalengeze kuti anthu ayambe kupha ndi kugulitsa ziweto zawo.

Matendawa amapha ng’ombe koma nanga nchifukwa chiyani aletsanso kuti nkhosa, nkhumba ndi mbuzi zisamaphedwe?

“Nzoonadi, kuti matendawa amagwira maka ng’ombe, koma ziweto zinazi zili ndi kuthekera kofalitsa matendawa. Mwachitsanzo, nkhumba ndi imene ili pachiopsezo chachikulu kufalitsa matendawa.

“Pofuna kuti matendawa tiwamalize mosavuta, tidaletsadi kuti ziweto zinazi zisatuluke m’bomalo komanso zisaphedwe n’cholinga choti pasakhale kufalikira kwa matendawa,” adatero Chikungwa.

Iye adati ng’ombe ikagwidwa ndi matendawa, imatenga sabata ziwiri kuti iyambe kuonetsa zizindikiro zoti ikudwala. Ikagwidwa ndi zilonda za m’mapazi komanso kukamwa imalephera kuyenda ndi kudya ndipo zikatero imafa.

Malinga ndi ofesi ya ziweto muunduna wa zamalimidwe, boma la Nsanje lili ndi ng’ombe 40 000, mbuzi 147 000, nkhosa 3 000 ndi nkhumba zoposa 20 000.

Boma la Chikwawa nalo lidakhudzidwa ndi matendawa ndipo ng’ombe 91 965 ndizo zidalandira katemera m’chigawo choyamba cha katemerayo.

Matendawa adabuka mu December 2015 ndipo mwezi wa January boma lidalengeza kuti matendawa atha m’bomalo. n

Related Articles

Back to top button