Chichewa

DPP madzi afika mkhosi—Muntali

Listen to this article

Zipani zotsutsa zati n’zodabwa kuti boma lagundika kukweza anthu ogwira ntchito m’boma, komanso kulipira mafumu nthawi ino ya kampeni pamene mmbuyo monsemu akhala akudandaula koma samathandizidwa.

Mwezi umodzi wokha boma lakweza apunzitsi 20 000, apolisi 7 000 moti padakali pano lili mkati molipira mafumu 42 000 ndalama za miyezi 6 zomwe zidatsalira chaka chatha.

Otsutsa akuti chipani cha DPP chikunyengerera mafumu kuti adzachivotere

Boma ligwiritsa ntchito K832 miliyoni polipira mafumuwo.

Zipani zotsutsa zati zikuona kuti chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) chikungofuna kugwiritsa ntchito ndondomeko zaboma pochita kampeni.

Koma mneneri wa boma Henry Musa adati sakuonapo vuto lililonse chifukwa palibe lamulo lomwe limafotokoza nthawi yokwezera anthu pantchito kapena kulipira mafumu.

 “Anthu ogwira ntchito m’boma akhala akukwezedwa, komanso mafumu akhala akulipidwa m’maulamuliro onse omwe akhalapo.

“Choseketsa n’choti palibe lamulo lomwe lifotokoza nthawi yokwezera ogwira ntchito kapena kulipilira mafumu,” adatero Mussa.

Mfumu Chindi ya ku Mzimba, Chadza ya ku Lilongwe ndi Dambe ya ku Neno yatsimikizira Tamvani kuti mafumu alandira mswahara wa June mpaka December 2018.

Mneneri wa unduna wa maboma ang’onoang’ono ndi chitukuko cha m’midzi Muhlabase Mughogho adati ndalamazi n’zomwe boma limayenera kuonjezera pa mswahara wa mafumuwo kuchokera pomwe Nyumba ya Malamulo idakweza mswaharawo.

“Nyumba ya Malamulo idavomereza kuti mswahara wa mafumu ukwere ndi K100 pa K1 000 iliyonse koma kuyambira mwezi wa June mpaka December 2018, mafumu samalandira ndalama yoonjezerayo ndiye akupatsidwa pano,” adatero Mughogho.

Mlembi wamkulu wa chipani cha UTM Patricia Kaliati adati ndiwodabwa kuti kuonjezera mswahara wa mafumu kutavomerezedwa, aphungu adaika m’bajeti ndiye n’chifukwa chiyani samapatsidwa ndalama zonse?

“Apatu ndikuona kuti boma limazunza dala mafumu kuti pambuyo pake adzawatseke m’maso nthawi ya kampeni. Uku n’kulakwa chifukwa panthawiyo akadatha kupanga ndondomeko zina,” adatero Kaliati.

Koma iye adati ndiwokondwa kuti mafumuwo alandira ndalama zawo zomwe adagwirira ntchito ngakhale azilandira nthawi yolakwika.

Kaliati adati ndalamazo n’zofunika kuonjezeranso chifukwa n’zochepa poyerekeza ndi ntchito yomwe mafumu amagwira.

Mawuwa akugwirizana ndi omwe adalankhula mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress (MCP) Lazarus Chakwera pa msonkhano wake wa ku Kasiya kuti mswahara wa mafumu ndiwofunika kuganiziridwa, komanso azipatsidwa mu nthawi yake.

Mneneri wa MCP Maurice Munthali adati zomwe zikuchitikazi zikusonyeza kuti chipani cha DPP chapanikizika chifukwa cholephera kuchita zinthu mu nthawi yake.

“Kodi aphunzitsi amayenera kukwezedwa liti? Nanga mafumu amayenera kulandira liti ndalamazo? Panopa madzi ali mkhosi ndiye akufuna awanamize? Ayi sititero,” adatero Munthali.

Iye adati aphunzitsi ndi apolisi omwe akwezedwawo awonetsetse kuti zofunikira zonse zatheka kuti wina asadzawakanire mawa, komanso mafumu alandire ndalama zawo koma zisawasokoneze pokavota,” adatero Munthali.

Mlembi wamkulu wa chipani cha United Democratic Front (UDF) Kandi Padambo adati boma lifotokozere bwino mafumu ndi anthu komwe kwachokera ndalamazo chifukwa ena akhoza kumaona ngati DPP ndiyo yapereka.

Katswiri pa ndale George Phiri adati Mussa akunena zoona kuti palibe lamulo lofotokoza nthawi yokwezera munthu kapena kumulipira malipiro ake, koma pali ndondomeko zina zomwe zimayenera kutsatidwa zomwe akuona kuti sizidatsatidwe.

“Choyamba munthu amakwenzedwa akagwira bwino ntchito. N’zowona kuti aphunzitsi ndi apolisi onsewa akugwira bwino ntchito yawo? Chachiwiri adziwa liti kuti akuyenera kukwenzedwa pa ntchito?” adatero Phiri.

Iye adati nkhaniyi ikapanda kuunikidwa bwino, idzabweretsa mavuto aakulu patsogolo makamaka ngati sipakhala makalata a umboni oti anthu akukwezedwadi pa ntchito.

Related Articles

Back to top button