Chichewa

Dyson Gonthi: Msangalatsi wa pakanthawi

Kwa amene tidabadwa pakanthawi Dyson Gonthi ndilo dzina limayambirira kubwera mumtima tikamva ting’oma ndi kanyimbo ka Nzeru Nkupangwa komanso ambiri tamumvapo akuwerenga ndi kuulutsa mawu pawayilesi ya boma ya Malawi Broadcasting Corporation (MBC-Radio 1). Zambiri za mkuluyu zidakhala ngati zidakwiririka kaamba ka kukula n’kupuma pazochitika.

STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere:

 

Gonthi:  Zisudzo ndidayamba kalekale
Gonthi: Zisudzo ndidayamba kalekale

Tikudziweni bwana.

Dzina langa ndi Dyson Gilbert Gonthi, ndimachokera m’mudzi mwa Kasiya kwa Mfumu yaikulu Chilooko m’boma la Ntchisi. Kunena za maphunziro aaah, sindidapite patali… ndidalekezera Fomu 4 pa Robert Blake ku Dowa m’chaka cha 1966.

Nanga mbiri yanu ya ntchito ndi yotani?

Ntchito ndidayamba m’c h a ka cha 1966 nditangomaliza sukulu. Ntchito yanga yoyamba idali yogula mbewu kumsika wa Admarc ku Nasawa. Nditagwirako pang’ono, ndidaganiza zokapitiriza maphunziro ndiye ndidauyamba ulendo wa ku Uganda koma ndidabwererera ku Norton m’dziko la Zimbabwe chifukwa cha zovuta zina makamaka zikalata zoyendera. Nditabwerera, ndidalowa m’boma kunthambi ya zofalitsa nkhani ya Malawi News Agency (MANA) m’chaka cha 1967. Ndidagwira kumeneku mpaka m’chaka cha 1970 pomwe ndidapita ku MBC mpaka kupuma koyamba.

Mukutanthauzanji mukati kupuma koyamba?

Ndikutero chifukwa m’c h a ka cha 1993 ndidabwereranso ku MBC komweko komwe ndidagwira mpaka m’chaka cha 2006 pomweno ndidapumiratu chifukwa cha kukula.

A n t h u a k h a l a n s o akukumvani mukuchita zisudzo, mungatiuzepo zotani pamenepa?

N’zoonadi ndimapanga zisudzo ndipo ndidayamba kalekale ndili wamn’gono. Ndikakhala pakati pa anzanga ndimakhala msangalatsi wawo ndiye ndidaona kuti ndingopitiriza kuchita zisudzo. Pachifukwa ichi ndidayambitsa gulu langa la zisudzo la DYGO Drama Group potengera dzina langa la Dyson Gonthi, komaso ndachitapo z isudzo ndi magulu osiyanasiyana pawayilesi ndi m’malo ena.

Munganeneponji pa za zisudzo muno m’Malawi?

Zisudzo ndi luso lomwe latenga nthawi yaitali kuti anthu alivomere ngati njira yoti munthu akhoza kumakhalira m’moyo mwake. Ndimakumbuka kalelo makolo amatikalipira mwinanso kumenya kumene tikamachita zisudzo. Ankati zikhoza kutisokeretsa m’moyo wathu. Komano zina kambu zina leku, zisudzo n’zabwino ndipo kwa masiku ano anthu akupanga ndalama ndi zisudzo. n

 

Related Articles

Back to top button