Nkhani

Dz Young Soccer, ‘Mighty’ adutsa

Chikho cha Standard Bank chayamba ndi moto pamene matimu a asirikali a Kamuzu Barracks ndi Mafco FC aona msana wa njira atakwapulidwa ndi Dedza Young Soccer FC komanso Be Forward Wanderers kudzera m’mapenote.

Chikho cha K10 miliyonichi chidayamba modabwitsa Lachitatu pamene timu ya Kamuzu Barracks idaona mdima pa Civo Stadium itachitidwa chiwembu ndi Dedza Young Soccer kudzera m’mapenote. Masewerowo adathera 2-2 ndipo nthawi ya mapenote Young Soccer idalimba chifu pokakamizabe asirikaliwa kuti atuluke m’chikhochi. 10 kwa 9 ndi momwe mapenotewo adathera, kukomera anyamata a ku Dedza.

Lachinayi udalipoliponso pabwaloli Wanderers kulimbana ndi asirikali a Mafco.

Masewerowanso adatheranso m’mapenote atalepherana duu kwa duu ndipo Wanderers idapuntha Mafco 4-3 m’mapenotewo.

Mafco idali ndi mwawi wambiri moti ikadatha kuchinya zigoli m’phindi 90 koma zonse zidangothera hiii!

Iyitu idali ndime yachipulula ndipo matimu amene achita bwinowa alowa m’ndime ya makotafainolo. Apa ndiye kuti Dedza iphana ndi Civo m’ndimeyi pamene Wanderers ikumana ndi Red Lions.

M’makotafainolo ena, timu yomwe ikuteteza chikhochi, Silver Strikers, ikwapulana ndi Blue Eagles pamene Moyale Barracks ikumana ndi Big Bullets.

Kochi wa Wanderers Elia Kananji adati ali ndi chiyembekezo kuti timu yake ichita zakupsa m’chikhochi.

“Adali masewero ovuta koma Mulungu adali mbali yathu. Tikukhulupirira kuti Mulungu yemweyo akhala nafe mumpikisanowu mpaka kumapeto,” adatero Kananji.

Naye Pofera Jegwe, kochi wa Dedza Young Soccer, adati kupambana kwawo ndi chithokozo kwa masapota awo.

“Mukudziwa kuti tidachita kuvoteredwa kuti tisewere m’chikhochi, ndiye kupambanaku ndi njira imodzi yothokoza amene adativoterawo,” adatero Jegwe.

Bungwe la FAM lomwe likuyendetsa mpikisanowu litulutsa masiku amene makotafainolowa aseweredwe.

Related Articles

Back to top button