Nkhani

Dziwani za matenda a mphere

Listen to this article

Kutsatira malipoti a kubuka kwa matenda a mphere kuchigwa cha mtsinje wa Shire, uyu ndi tsatanetsatane wa matendawa kuchokera pa zomwe bungwe loona za umoyo padziko lapansi la World Health Organization lidapeza.

Matenda a mphere amakhudza khungu la munthu ndipo amayambika ndi kachilombo kakang’ono kamene kamapezeka muchakudya. M’chingerezi,

Scabies_Fingerskachilomboka kamatchedwa ‘mite’ ndipo asayansi amakatcha Sarcoptes scabiei.

Kachilomboka sikaoneka chifukwa ndi kakang’ono kwambiri. Kakalowa pakhungu la munthu, amakanda mosalekeza.

Malinga ndi World Health Organization, matenda a mphere amati ndi okhudzana ndi madzi. Ndi zosadabwitsa kuti lero tikukamba za mphere zomwe zafala kuchigwa cha mtsinje wa Shire komwenso madzi aononga katundu ndi kugwetsa nyumba.

Matendawa amafala ngati kachilomboko kapita pakhungu la munthu wina

koma amafala kwambiri pamene munthu amene wakhudzidwa ndi matendawa wakhudzana ndi mnzake monga pogonana mosadziteteza.

Matendawa amafala kwambiri moti mu 2010 anthu oposera 100 miliyoni

padziko lapansi ndiwo adakhudzidwa ndi matendawa.

Matendawa mungawadziwe msanga chifukwa pamene akuyamba umangokanda mosalekeza ndipo khungu limatha kusupuka. Zizindikiro zokhala ngati

walumidwa ndi udzudzu zimaoneka.

Kukandaku kumafika palekaleka usiku pamene ukugona. Kuyabwakutu

kumachitika chifukwa tizilombo tija timakhala tikuyendayenda m’thupimo.

Matendawa amafalanso posinthana zovala, zopukutira mukasamba, zofunda. Koma

matendawa angathe kukhala pathupi la munthu kwa masiku atatu osapatsira munthu.

Kugwiritsira ntchito mankhwala monga permethrin kapena ivemectin kumachepetsa kufala kwa matendawa koma mpaka lero palibe mankhwala amene amachiza matendawa.

Kukhala munthu wa ukhondo kungathandize kuti usadwale matendawa. Izi ndi zomwe achipatala amalimbikitsa kuti muyenera kumasamba, zovala zizikhala zochapa ndipo malo ogona akhale okonzedwa bwino.

Related Articles

Back to top button
Translate »