Nkhani

Eid al Adha: Chikondwerero chopereka nsembe

Listen to this article

Chaka ndi chaka a chipembedzo cha Chisilamu amakhala akuzinga ziweto nthawi ina. Pa mwambowu, Asilamu amakhala akutsatira zomwe Mulungu adalamula Abraham zaka zammbuyo. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Sheikh Malekano Rajab ndipo adakambirana motere:

Poyamba, ndikudziweni….

Ndine Sheikh Malekano Rajab ndimatumikila pamzikiti wa pamsika wa Area 22 ku Lilongwe.muslims

Kodi chaka ndi chaka Asilamu amakhala ndi mwambo wopha ziweto talongosolani kuti zimakhala bwanji?

Mwambo umene uja timakhala tikukumbukira zomwe Mulungu adauza Abrahamu kalelo nthawi yomwe adavomera kupereka mwana wake Ishmael nsembe. Akuti azipereka mwanayo nsembe, Mulungu adatumiza nkhosa ndipo mwanayo adapulumuka. Mulungu adalamula Abrahamu kuti chaka chilichonse Asilamu azikhala ndi mwambo umenewu ngati chikumbutso komanso kulemekeza Mulungu.

Mwambowu umachitika liti?

Umachitika tsiku la khumi (10) la mwezi wa chisanu ndi chinayi m’kalendala ya Chisilamu. Pakafika pa 1 mwezi umenewo msilamu aliyense amayenera kuyamba kusala kwa masiku 10 ndipo kusalako kumatha tsiku la nambala 10 lomwe kumakhala kuzinga ziweto kapena chikwenderero cha Eid al Adha. Chimachitika nchiyani pa tsikuli?

Msilamu amayenera kugula chiweto monga ng’ombe kapena mbuzi nkupha. Nyama yake nkugawa koma naye mwini wake amayenera kutengapo gawo osangogawa yonse ayi. Kupha nyamako kumatchedwanso Qrubani.

Chiweto chake chimayenera kukhala chotani?

Chiweto chikhoza kukhala chilichonse koma chikhale chopanda chilema kapena choti chidakokako ngolo kapena chidalimako. Chikhale chiweto chalunga ndipo chopanda ngakhale chilonda pathupi lake komanso chathanzi.

China chimachitika nchiyani?

Lisadafike tsikulo, Asilamu a ndalama zawo amapita ku Mecca. Ulendo wopita ku Mecca umatchedwanso kuti haji ndipo ndi imodzi mwa nsanamira za Chisilamu. Omwe alibe ndalama amakhala kumudzi koma nawonso amakhala akutsatira zoyenera kuchita kuti tsikulo lisadetsedwe.

Nanga wina akaphonyetsa monga kupha chiweto chodwala zimakhala bwanji?

Pamenepo nsembe imeneyotu siyilandiridwa chifukwa ndiyodetsedwa ndipo ndiyosayenera kuperekedwa kwa Mulungu. Nthawi zonse munthu amayenera kukumbuka kuti iyi ndi nyengo yoyera yoyenera kuyeretsedwa.

Nanga aja amakhala akuimbawa amatinji?

Amene aja sakhala akuimba nyimbo, amakhala akupemphera pemphero lomwe mngelo Gabriel ankanena akudzapereka nkhosa yomwe Abrahamu adasinthitsa ndi mwana wake yemwe adakonzeka kukamupereka nsembe. Pemphero lake limati Mulungu ndi wamkulu palibe ofanana naye ndipo iye ndiye tate basi.

Nanga ochepekedwa ndalama sizingatheke kugula nyama yophaipha nkugawa?

Ayi sizingatheke pamafunika kuchita kupha ndithu. Kugula ndi kugawa yophaipha ndiye kuti sikhalanso idi koma sadaka. Komanso umayenera kupha tsiku lenilenilo kapena masiku atatu otsatira kupanda apo, imeneyonso ndi sadaka odati idi ayi.

Ndiye mwati zidayamba liti?

Zidayamba kalekale nthawi ya Abrahamu pomwe Mulungu adamuuza kuti mwezi wa nambala 9, kuyambira pa 1 ndipo tsiku la nambala 10 kuzichitika mwambo oterewu. Kuchoka pa Abrahamu, aneneri onse omwe ankabwera kufikila pa Muhammad amatsatira zimenezi ndiye Asilamu onse amayenera kutsatira.

Zimasiyana bwanji ndi Idi ina ija?

Ina ija, Eid al Fitr, ndi idi yosala timayenera kusala masiku 30 chifukwa Mulungu adamuuza Abrahamu kuti munthu aliyense amayenera kusala. Ngakhale Yesu adasala masiku 40 m’chipululu ndipo aneneri ena onse 124 000 amasala ndiye ife tilekerenji? Tayenera kusala ndikutsatira chiphunzitso chomwe adatisiyira aneneri athu kuchoka kwa Mulungu wathu.n

Related Articles

Back to top button