Nkhani

Esiteti, anthu ayanjana pa za malo

Listen to this article

Esiteti ya Lujeri yalola anthu pafupifupi 5 000 amene adalowerera malo a esitetiyo ku Mulanje kuyambira zaka za m’ma 2000 kukhala pamalowo popanda zovuta zilizonse.

Mkulu wa bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiative (Cdedi) Silvester Namiwa wati wakondwa chifukwa esitetiyo yalola kulekera anthuwo malowo, pomwe bungwelo likupitiriza kumenya nkhondo kuti anthu a ku Thyolo ndi Mulanje apezenso malo amene atsamunda adawalanda.

Namiwa: Anthu akupambana nkhondo

“Takondwa kuti a Lujeri alola kumvana ndi anthuwo. Apa zikusonyeza kuti pang’onopang’ono nkhondoyi anthu apambana,” adatero a Namiwa.

Malinga ndi amene amaimira anthuwo pamlandu umene udali kubwalo lalikulu, a Charles Kusiwa adati chimkulirano pakati pa anthuwo ndi esitetiyo udadza pomwe anthuwo adalowerera kumpoto ndi kummawa kwa esitetiyo. Esitetiyo siyimafuna kupereka malowo kwa anthu pomwe anthuwo nawo samafuna kuchoka.

“Pa 23 December chaka chatha, esitetiyo idapita kukhoti n’kukasumira agulupu a Gladstone, T/A Njema ndi 10 ena, kuwadzudzula kuti alowerera malo a esiteti,” adatero a Kusiwa.

Woweruza kubwalo la milandu lalikulu Mike Tembo ndiye adakhala pakati pa esitetiyo ndi anthuwo ndipo adanenetsa kufunika kwa chiyanjano pakati pa eni esiteti komanso anthu a m’deralo. Zokambirana zidatenga maola asanu kufika adagwirizana kuti esitetiyo isathothe anthuwo.

“Woweruza adanenetsa kuti anthu adalowerera kale malowo ndipo adamanga kale pokhala ndipo adabzala mbewu ya tiyi choncho kuwathotha kukadangobweretsa mavuto ena,” adatero a Kusiwa.

Nkhani ya malo imavuta kwambiri m’maboma a Mulanje ndi Thyolo kumene alo ambiri ali m’manja mwa maesiteti a tiyi ndi khofi. Mmbuyomu a Vincent Wandale aali kumenyera kuti mabomawo akhala dziko palokha kuti nkhaniyi athane nayo.

Related Articles

Back to top button
Translate »