Nkhani

FAM ndi Kamuzu Stadium

Listen to this article

Sabata yatha kwathu kuno kudabwera alendo a Fifa kudzayendera bwalo la Kamuzu Stadium ngati ndi loyenera kuti mipikisano ya chikho cha World Cup iziseweredwapo.

Tidali ndi nkhawa kuti basi bwaloli alikana malinga ndi momwe likuonekera. Mukudziwanso paja kuti bwaloli lili ndi mavuto ambirimbiri.Bullets-1

Koma zidali zodabwitsa kumva akuti bwaloli lakhoza mayeso, kusonyeza kuti masewero a Malawi ndi Tanzania achitikira pomwepa.

Ife titapita kubwaloli, tidakapeza kuti a FAM akonza zingapo. Adasesapo komanso adakonza malo omenyera mapenote.

Alendowa, omwe adachokera ku Tunisia ndi Zambia, adangoona malo omenyera mapenote momwe akongolera. Kudzaonanso kuti zitsotso zonse asesa basitu adangoti choongu!

Hahaha! Mpira ku Malawi sudzatheka. Boma lidakachitako manyazi abale. Izitu n’zachisoni.

Bwaloli latha, tinene mosapsatira. Pena kukumakhala kulibe madzi moti aganyu akumadzithandizira m’chikatoni.

Waya wa malire ndi posewerera adagwetsadwa kalekale moti masapota ataganiza zolowa m’bwaloli mpira uli mkati angathe kuzichita ndipo zakhala zikuchitika.

Benchi ija idathyokathyoka ndipo adachita kubwerekera benchi ya ku Chiwembe kuti bwaloli likhoze mayeso.

Dziko lino lidakachitako manyazi, abale! Bwalo lija likupanga ndalama zambiri zomwe zikupita kuboma.

Boma litangonena kuti ndalama zopangidwa pa Kamuzu Stadium zisamapite m’thumba la boma ndipo zithandizire kukonzera bwaloli, bwezi litakonzedwa kalekale.

Chinthu chikukupangirani ndalama koma osafuna kuchikonza. Kodi sitikhumbira mabwalo a anzathu kunja kuno?

Related Articles

Back to top button
Translate »