Nkhani

Fisi wadya mayi wa ku Tsangano

Listen to this article

Anthu a m’mudzi mwa Doviko, Mfumu Mpando, m’boma la Ntcheu, akukhala ndi mantha chifukwa cha afisi omwe akuzunguza m’deralo.

Loweruka lapitalo usiku afisiwo adadya mayi wa zaka 56 yemwe adamupeza atagona pa njira pochoka ku bibida.

Pamene anthu a m’mudzimo amathamangira ku maloko kukayesa kupulumutsa mayiyo, adapeza khamu la afisi litamupha kale.

Mneneri wa apolisi m’boma la Ntcheu, Hastings Chigalu, adauza Msangulutso kuti mayiyu, Ellenita Zembeleni, amakonda kupita ku mowa ndi mwamuna wake wa zaka 74, Emiliano Kwaderanji.

Iye adati koma patsiku la tsokali mwamuna wakeyo adachokako msanga ku mowako, n’kumusiya mkazi wake mmbuyo.

Chigalu adati mayiyu adachokako ku mowako nthawi ili m’ma 11 koloko usiku ali yekhayekha ulendo wobwerera kunyumba, osadziwa kuti m’mudzimo afisi alusa.

“Chifukwa cha mphamvu ya mowa Zembeleni adakanika kukafika kunyumba kwake ndipo adagona patchire lina m’mudzimo,” adatero Chigalu.

Iye adati apa mpamene fisi adamuona n’kuyamba kumuluma.

“Zembeleni adakuwa mpaka mnyamata wina wa m’mudzi adamva ndikuthamangira kutchireko kukayesa ku ndikuthamangitsa fisiyo,” adatero Chigalu.

Iye adati mnyamatayo ataona kuti fisiyo wathawa adamathamangira m’mudzi kukadziwitsa anthu.

Pamene khamu la anthu a m’mudzimo limafika, lidapeza atafa kale popeza fisiyo adadya mbali yaikulu ya thupi lake.

“Anthu andangotenga ziwalo zotsala za mayiyo popeza fisiyo adadya mbali yaikulu,” Chigalu adatero.

Aka sikoyamba afisi kuvuta m’boma la Ntcheu chifukwa m’chaka cha 2018 adadulanso mikono ya mwana wa zaka 11 ndi kuvulaza anthu ena atatu.

M’modzi mwa anthu a m’mudzimo yemwe sadafune kutchulidwa dzina adavomerezana ndi apolisi kuti mayiyo adadyedwa atagona panjira kuchokera ku mowa.

Mfumu Mpando yati mudzi womwe mwachitika ngoziyi uli pafupi ndi phiri.

Mfumuyi idati afisiwo amachokeranso m’mapanga a m’dziko la Mozambique pafupi ndi Tsangano.

Mkulu wa nthambi yoona za malo wosungirako nyama zakutchire, Bright Kumchedwa, adati nthambi yake itapita ku maloko siidapezeko afisiwo koma kafukufuku waonetsa kuti amayendera pakati pa dziko lino ndi la Mozambique.

“Zikuonetsa kuti afisiwo abwerera ku Mozambique, koma tapempha anzathu a African Parks kuti akadzabwerera, tidzawagwire n’kuwapititsa ku nkhalango zotetezedwa,” Kumchedwa adalongosola.

Related Articles

Back to top button
Translate »