Chichewa

Flames itenga mwezi ikukonzekera Guinea

Listen to this article

 

Timu ya mpira ya dziko lino ya Flames itenga mwezi umodzi ikukonzekera masewero ake ndi Guinea omwe adzachitike mwezi wa March chaka chino mumpikisano wa Africa Cup of Nations.

Malinga ndi pulezidenti wa bungwe loyendetsa za mpira m’dziko muno la FAM, Walter Nyamilandu, Flames idzayamba zokonzekerazi kumayambiriro a mwezi wa mawa.

Flames iyamba kukonzekera mwezi wa mawa
Flames iyamba kukonzekera mwezi wa mawa

Nyamilandu wati timuyi yapatsidwa mwezi umodzi yazokonzekera chifukwa osewera ambiri ali pa tchuthi malinga ndi kutha kwa ligi ya TNM Super League.

“Monga mukudziwa tili ndi masewero akulu mu March chaka chino pomwe tikumane ndi Guinea. Potengera ndi zimene mphunzitsi watimuyi, Ernest Mtawali adapempha ku FAM, taona kuti nzofunika kuti tovomere zoti timuyo ikhale ikukonzeka nthawi yaitali. Paja osewera ambiri akupuma chifukwa TNM Super League yatha. Izi zikuonetseratu kufunika kotenga nthawi yaitali tikukozekera,” adatero Nyamilandu.

Padakalipano, FAM yaloleza kuti mphunzitsi wa timu ya dzikolinoyo apite ku South Africa komwe akaunike ena mwa osewera a dziko lino kuti akhale nawo mutimu yomwe ikumane ndi Guinea.

Ena mwa osewerawa ndi Atusaye Nyondo yemwe amasewera mu timu ya Pretoria University ndi Robert Ng’ambi yemwe amasewera mu Platinum Stars amenenso ubale ndi Mtawali unada chifukwa

sanalowetsedwe pomwe Flames imakumana ndi Swaziland chaka chatha.

Mmodzi mwa akatswiri a mpira m’dziko muno Peter Mponda yemwe anali kaputeni wa Flames wayamikira FAM polola mphuzitsi wa timu ya dziko linoyo kupita kukaunika osewera omwe ali ku South Africa.

Iye watinso akadakonda kuti Mtawali akhalenso paubale wabwino ndi osewera ngati Ng’ambi chifukwa tchito zake ndizofunikirabe ku timuyi.

Flames ikuyenera kuwina masewero ake ndi Guinea pofuna kuti ichulukitse mwayi opitirira mumpikisanowu. n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »