Nkhani

Fodya wakunja wayamba kulowa

Listen to this article

Pomwe dziko la Malawi lalima fodya wochepa ndi makilogalamu 27 miliyoni pamlingo omwe ogula fodyayu adaitanitsa, mavenda ena amachawi ayamba kulowetsa fodya kuchoka m’maiko oyandikana ndi dziko lino.

Fodyayu akumalowetsedwa pogwiritsa ntchito njira zozemba chifukwa mchitidwewu  ngosemphana ndi malamulo a dziko lino.

Wogwirizira udindo wa mkulu wa bungwe loyendetsa ulimi wa fodya m’dziko muno la Tobacco Control Commission (TCC) David Luka adati bungwe lake likudziwa za mchitidwewu ndipo lidatumiza maofesala ake kumalo onse omwe izi zikuchitika.

“Maofesala athu ali ku Nkhamenya, m’boma la Kasungu komwe kumalowera fodya kuchokera m’dziko la Zambia ndipo ena ali ku Mchinji komanso ku Namwera m’boma la Mangochi komwe fodya wake amakhala ochokera ku Mozambique,” adatero Luka.

Iye adati bungwe lake ndi lokhumudwa ndi mchitidwewu omwe uli vuto lalikulu pa ulimi wa fodya m’dziko muno.

“Ntchito  yoyesetsa kuti fodya asalowe kapena kutuluka m’dziko muno siyapafupi, ndipo sikwapafupi kuchitapo kanthu” adatero Luka.

Iye adaonjezeranso kuti nkhanizi kwambiri ndi zokhudza dziko ndi dziko linzake.

Alimi a fodya ena m’boma la Mchinji adatsimikiza za kulowa kwa Fodya m’dziko muno.

Mmodzi mwa alimiwa, Lazarus Chitedze, yemwe wakhala akulima fodya kwa zaka pafupifupi 20 adati fodyayu akulowa pang’ono chabe kuchokera m’dziko la Zambia kusiyana ndi momwe zimakhalira zaka zonse.

“Akulowetsa fodya ndi mavenda ang’onoang’ono omwe amagwiritsa ntchito njinga, mwina chifukwa chakuti m’maliremu muli asilikali omwe akulondera chimanga kuti chisatuluke,” adatero Chitedze.

Iye adati chaka ndi chaka fodya amalowa kuchokera ku Zambiako kapena kutuluka kuchoka m’dziko muno.

“Zimatengera komwe msika uli bwino chaka chimenecho.Ngati ku Zambia zili bwino, mavenda amazembetsa fodya kupita naye komweko,” adatero Chitedze.

Iye adati zikatere zimawakomera alimiwa chifukwa mavendawa amawagula mokwera mtengo kusiyana ndi ku msika wa fodya.

Malinga ndi Chitedze, chiopsezo chimakhalapo fodya akamalowa kuchokera m’dzikolo chifukwa zikhonza kuchulutsa fodya pamsika kuposera mlingo omwe ogula akufuna.

Polankhulapo mlimi wina yemwe sadafune kutchulidwa dzina lake adati fodyayu akulowa pang’ono chifukwa ku Zambiako ayamba kumene kusankha fodya.

“Akangoti wafika pachimake kumeneko, timuona akulowa wochuluka zedi,” adatero mlimiyo.

Mwezi wathawu, woyan’ganira dera la kummawa m’boma la Zambia Chanda Kasolo adauza ena mwa atolankhani a dzikolo kuti asilikali omwe ali m’malire a dziko lino ndi dzikolo akutetezanso kuzembetsa fodya.

Dziko la Zambia lidalengeza chaka chathachi kuti likweza mlingo wa fodya yemwe amalima kuchoka pa ma kilogalamu 23 miliyoni kufika pa 30 miliyoni chaka chino.

Ndipo chaka chathachi mtsogoleri wa bungwe la alimi la Eastern Fodya Association of Zambia (Efaz) Franklyn Mwale adadandaulira bungwe loyendetsa ulimi wa fodya m’dzikolo kuti msika wawo amautsekula mochedwa poyerekeza ndi wa dziko lino.

Koma limodzi mwa mabungwe a alimi la Tobacco Association of Malawi (Tama) lidati silidalandire lipoti lililonse lokhudza kulowa kwa fodya kuchokera mdziko la Zambia.

Related Articles

Back to top button
Translate »