Chichewa

Fodya wobwerera kumsika amugulitsa

Listen to this article

Mkulu wa bungwe la Tobacco Association of Malawi (Tama), Graham Kunimba, wati fodya yemwe anabwerera pamsika chaka chino tsopano amugulitsa.

Iye adati ngakhale zinthu zinavuta, bungwelo lidayesetsa kukambirana ndi boma, bungwe la Tobacco Control Commission (TCC) ndi ogula kufikira tsopano fodya yense amugulitsa. Mwa magawo 100 alionse a fodya wofika kumsika, 70 akhala akubwezedwa chaka chino, ndipo alimi ambiri manja anali mkhosi kusowa chochita naye.

Alimi a fodya ngati uyu ayenera kukhala ndi zitupa

Kunimba wati malonda a fodya m’chakachi anavuta kwambiri chifukwa fodya analimidwa wochuluka kwambiri kuposa mlingo omwe ogula amafuna. Kafukufuku akusonyeza kuti dziko la Malawi limayenera kulima fodya okwana makilogalamu 158.1 miliyoni koma chaka chino tinakolola makilogalamu 205.53 miliyoni.

“Ngakhale fodyayu amugula, mitengo yake inali yotsika kwambiri. Izi zapangitsa kuti dziko lino lipeze ndalama zochepa ku ulimiwu kusiyana ndi chaka chatha. Kafukufuku akusonyeza kuti chaka chatha dziko la Malawi lidapeza K216.8 biliyoni kuchokera ku fodya, koma chaka chino tapeza K162.6 biliyoni.

“Pamenepa ndiye kuti boma lapeza ndalama zochepa komanso msonkho wochokera ku ulimiwu wachepa ndipo mwachidziwikire chuma cha  boma chakhunzidwa,” adatero Kunimba.

Mkulu wa bungwe la Farmers Union of Malawi (FUM), Alfred Kapichira-Banda, wavomereza za kugulitsidwa kwa fodyayu ndipo adati fodyayu amugula mongolanda. “Fodya wambiri amugula pamtengo wa K553 pa kilogalamu ndipo wina amugula kuchepera apo,” adatero Kapichira-Banda.

Mmodzi mwa alimi omwe anakhudzidwa ndi vutoli, Isack Banda wa m’boma la Dowa, wati zomwe wakumana nazo m’chakachi zayamba kumupatsa maganizo osiya ulimiwu chifukwa sanapeze phindu lililonse.

“Ulimi wa fodya umalowa zambiri komanso umalira zipangizo zochuluka ndi zokwera mtengo moti ndikawerengetsa zonsezi palibe chimene ndaphula koposa ndingoleka,” adatero Banda.

Bungwe la Tama likuchenjeza kuti mlimi amene sanalandire chilolezo kuchokera ku TCC asalime fodya chifukwa sadzagulidwa kumsika.

Bungweli lati izi zithandiza kuti fodya yemwe alimidwe chaka chino asapyole mlingo omwe dziko la Malawi likuyenera kulima. Kunimba adati alimi omwe alandira chilolezochi apatsidwa mlingo wa fodya yemwe akuyenera kulima.

“Tikuwalangiza alimi onse kuti asatire mlingo omwe TCC yawapatsa ndipo asapyole, kuopa kuchulutsa zokolola zomwe zingapangitse kuti malonda adzavutenso chaka chamawachi,” adatero Kunimba.

Ngakhale fodya adakumana ndi mikwingirima yotereyi m’chakachi, amathandiza kwambiri ku chuma cha dziko lino ndi magawo 60 pa 100 aliwonse ndipo kufikira pano palibe mbewu yomwe ikupikisana naye ku nkhani imeneyi

Related Articles

Back to top button
Translate »