Chichewa

Gayighaye Mfune: Wosula oimba

Kuimba ndi luso lomwe ena amabadwa nalo pomwe ena amachita kuphunzira. Maphunziro a zoimbaimba amachuluka zifanifani ndipo zimatengera luso la mphunzitsi kumasulira zifanifanizo kuti ophunzira amve. Mathews Gayighaye Mfune ndi mmodzi mwa akatakwe ophunzitsa zoimbaimba ndipo amayendetsa sukulu ya zoimba ya Music Crossroads Malawi. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere:

Tidziwane, akulu.

Mfune: Ndimafuna kuti oimba apite patali
Mfune: Ndimafuna kuti oimba apite patali

Ine ndine Mathews Gayighayi Mfune ndipo ndimachokera m’mudzi mwa Chipofya kwa

T/A Katumbi m’boma la Rumphi. Ndili ndi digiri ya zamaphunziro yomwe ndidatenga ku University of Malawi. Ndidapanganso dipuloma ya zachikhalidwe ku South Africa. Ndidagwirapo ntchito ku unduna wa zamasewero ndi chikhalidwe ndipo pano ndikuyendetsa sukulu ya zoimbaimba ya Music Crossroads Malawi.

 

Mumawoneka kuti muli ndi luso la zoimbaimba, kodi mudaphunzira kuti?

Kuimba ndi mbali ya chibadwa changa komanso ndidazolowera kucheza ndi oimba, otukula oimba ndi ojambula nyimbo ku Malawi kuno komanso m’maiko akunja. Kuunduna wa zamaswero ndi chikhalidwe, ndinkayendetsa za luso loimba ndi zisudzo komanso maphunziro omwe ndidachita ku South Africa adandiika patali kwambiri.

 

Tandiuzeni mbiri ya Music Crossroads.

Limeneli ndi bungwe lomwe si laboma komanso si bizinesi ayi. Lidakhazikitsidwa m’chaka cha 2007 kuti liziphunzitsa achinyamata zoimbaimba. Bungweli limaphunzitsa oyimba oposa 500 pa luso loimba kudzera m’mipikisano ndi maphunziro a tsiku ndi tsiku. Kupatula kuphunzitsa achinyamata kuimba, timaphunzitsanso akaidi za matenda a Edzi, kuimba, kujambula ndi kupanga zimbale. Mwachidule ndife nthambi ya Jeunnesses Musicale International (JMI).

 

Masomphenya anu pa nkani yoimba muno m’Malawi ndi otani?

Ndimafunitsitsa kuti oimba athu adzafike patali ngati oimba a m’maiko ena komanso anthu adzayambe kuzindikira kuti kuimba ndi ntchito yandalama zambiri kuti adzakhale ndi ludzu lotukula zoimbaimba.

 

Zina mwa zomwe Music Crossroads Malawi idakwaniritsapo ndi ziti?

Taphunzitsapo aphunzitsi a m’sukulu za pulayimale ndi achinyamata kaimbidwe ka zida zosiyanasiyana, komaso timaphunzitsa achinyamata am’ndende luso losiyanasiyana. Achinyamata omwe timaphunzitsa akhala akupambana m’mipikisano ikuluikulu yokhudza maiko akunja komanso oimba ambiri omwe mumawadziwa ndi kuwamvera panowa adutsa m’manja mwa Music Crossrossroads Malawi. n

Related Articles

Back to top button