Chichewa

‘General Kanene’ watuluka m’ndende

Listen to this article

Mtsogoleri wa dziko la Zambia Edgar Lungu wakhululukira ndi kulutsa mundende General Kanene, woimba wotchuka m’dzikolo, yemwe dzina lake lenileni ndi Clifford Dimba.

Ndi mfulu tsopano: General Kanene
Ndi mfulu tsopano: General Kanene

Ndipo Lungu walangiza General Kanene kuti akhale kazembe pantchito zolimbana ndi mchitidwe wochita zachisembwere ndi ana ochepa misinkhu m’dzikolo.

Malinga nyuzi ya pa Intaneti yak u Zambia yotchedwa Tumfeko.com, General akuti walonjeza Pulezidenti Tembo kuti sadzamukhumudwitsa pantchito yomwe wamupatsa.

Bungwe la azoimbaimba la Zambia Association of Musicians (ZAM) akuti lalandira kumasulidwa kwa Gneral Kanene ndi manja awiri, makamakanso kuti wapatsidwa udindo wa ukazembe kufalitsa uthenga wa kuipa kogwiririra ana kudzera m’nyimbo zake.

Chaka chatha, bwalo la milandu lidagamula woyimbayu kuti akagwire ukayidi wa zaka 18 atamupeza wolakwa pamlandu wogwiririra mtsikana wazaka 14.

Iye amasewezera ukayidi wake pa Mukobeko Maximum Security Prison.

Atangokhala kundende kwa miyezi yowerengeka chabe, General Kanene adapeka nyimbo zingapo momwe akufotokoza za mazunzo omwe ankakumana nawo kundendeko.

Iye ankachenjezanso anthu ena kuti asazayerekeze kuphwanya malamulo kuti asakaone zomwe iye wadutsamo.

Related Articles

Back to top button