Chichewa

Gondwe azaza pamsonkhano

Listen to this article

 

Nduna ya za chuma Goodal Gondwe Lolemba idazaza pamwambo wosayinirana pangano la ngongole ndi banki ya zachitukuko mu Africa ya African Development Bank (AfDB) itazindikira kuti akuluakulu a kuundunawu sadabweretse mapepala osayinira panganolo.

Ndunayi imayembekezera kusayinira pangano la ndalama zokwana US$22 miliyoni (pafupifupi K16 biliyoni) mmalo mwa boma ndi oyimilira bankiyi Andrew Mwaba ku likulu la undunawu ku Lilongwe.

Adakwiya: Gondwe

Cholinga cha ndalamazi nkupititsira  ntchito za ulimi patsogolo ndi kutukulira achinyamata paulimi.

Gondwe adakhumudwa ndi kulephera kwa akuluakulu a kuundunawu kuzindikira kuti mwambowo udayamba palibe mapepala ofunikirawo ndipo adadula mkamwa oyendetsa mwambowo Alfred Kutengule kuti za mapepalawo zilongosoke.

“Zitheka bwanji kusayinirana pangano popanda mapepala ofunikira? Tisayina pati? Mapepala ali kuti apa?” Adafusa Gondwe.

Ndunayi itangolankhula izi, kudali yakaliyakali akuluakuliwo kuthamangathamanga mmawofesi kusaka mapepalawo kuti mwambo upitilire ndipo pomwe mapepalawo amapezeka, makina achinkuza mawu omwe amagwiritsidwa ntchito pa mwambowo adasiya kutulutsa mawu.

Izi zidangowonjezera kukhumudwa kwa ndunayi yomwe idangouza amisili olumikiza makinawo kuti asavutike nkugwiragwira  ndipo mwambowo ungopitilira popanda chinkuza mau kuti asunge nthawi yopitira ku Nyumba ya Malamulo. n

Related Articles

Back to top button