Chichewa

Gulani mbewu kwa ogulitsa ovomerezeka—Unduna

 

Unduna wa malimidwe walangiza alimi kuti ayenera kugula mbewu kuchokera kwa ogulitsa ovomerezeka okha poopa kugulitsidwa mbewu zoonongeka.

Mlembi wamkulu muundunawu, Erica Maganga, wati alimi aike patsogolo mbewu zopezeka m’sitolo komanso mabungwe amene adalembetsa ku undunawu.

Alimi ayenera kugula mbewu malo ovomerezeka okha
Alimi ayenera kugula mbewu malo ovomerezeka okha

“Kugulitsa mbewu popanda chilolezo chochoka ku undunawu ndi mlandu waukulu.

“Mbewu iyenera kugulitsidwa ndi okhawo ali pa mgwirizano ndi kampani zopanga mbewu.

“Ogulitsa mbewu otere amaphunzitsidwa bwino za kagulitsidwe ka mbewuzo komanso kasungidwe kake,” adatero Maganga.

Malinga ndi maganga, ogulitsa mbewu ovomerezeka amalandira chiphaso chogulitsira mbewu chomwe chimagwira ntchito kwa chaka chimodzi.

Iye adati onse ofuna kugulitsa mbewu ayenera kulembera kalata ku nthambi yoona za mbewu muundunawu ya Seed Certification and Control Unit.

“Ogulitsa amene sakwaniritsa ndondomeko zomwe amapatsidwa pogulitsa mbewu amalandidwa chiphasocho. Cholinga chachikulu n’chakuti alimi azigula mbewu zovomerezeka komanso zomwe sizidaonongeke,” adatero Maganga.

Related Articles

Back to top button