Nkhani

Gule wa utse ku Nsanje

Listen to this article

Mtundu ulionse umakhala ndi zinthu zokumbikira mtundu wawo kapena chikhalidwe. Umu zilinso choncho ndi mtundu wa Asena ku Nsanje komwe kuli gule wa utse. M’bomalo mudali mwambo wobzala mitengo, ndiye gule ameneyu adamuitana kuti asangalatse anthu. Abambo adafa ndi kuseka amayi akupukusa chiuno molapitsa. BOBBY KABANGO adali komweko ndipo adamuitananso kuti avine ndi mayi mmodzi. Atatha zonse, adacheza ndi mayi mmodzi motere:

Poimba amagwiritsa ntchito matabwa
Poimba amagwiritsa ntchito matabwa

Dzina ndani mayi?

Ndine Fakilesi Nachikadza, ndimachokera m’mudzi mwa Therere kwa T/A Malemia m’boma lino.

Gule wanji wokoma chonchiyu?

Ameneyu ndi utse. Utse ndi gule wa amayi okhaokha.

Atsikana saloledwa kuvina nawo?

Sangakwanitse kuvina. Guleyutu amafunika munthu amene angavine kwa nthawi yaitali osatopa, ndiye atsikana sangakwanitse koma ife akuluakulu.

Mumavina nthawi iti?

Timavina kukakhala zochitika monga kulonga mfumu, ndi zochitika zilizonse monga kubzala mitengoyi.

Mavinidwe ake ngotani?

Limakhala gulu la amayi okhaokha, ndiye timasema timatabwa ndipo aliyense amakhala ndi matabwa awiri amene amawamenyetsa kuti zizimveka bwino. Ena amakhala akuomba m’manja ndipo onse amaimba nyimbo. Mayi mmodzi amakhala akuduka m’chiuno. Iyeyu ndiye amaimirira pamene ena onse amakhala pansi. Amene akuvinayu amakhala ndi wenzulo yomwe amaimba.

Mutanthauza kuti amavina ndi munthu mmodzi?

Eya, koma tingathenso kumulandira chifukwa tonse timadziwa kuvina kwake.

Amavina bwanji?

Momwe ndikuchitiramu basi, nkhanitu ndi chiunochi kuchigwiritsa ntchito. Inuyonso tabwerani apa ndivine nanu kuti mukalembe zoona….eyatu ndi momwe timavinira guleyu.

Mudayamba liti kuvina guleyu?

Ine ndidabadwa ndipo ndidamupeza, timaonera makolo akuvina mpaka lero takula ndipo tikuvinanso.

Nyimbo mumaimba ija mumati chiyani?

Imeneyi ndi nyimbo yokamba za ubwino wa mitengo. Timati; azimayi tendene, aye! Azimaye tendene, tikabzale mitengo. Mafumu ali pomwepo, aye! Mafumu ali pomwepo tikabzale mitengo.

Pagulu ponsepa amene amavina bwino ndi inuyo?

Aliyense amavina bwino koma leroli anasankha ine kuti ndivine ndipo mwaonanso abambo ambiri akuyamikira kuti ndavina bwino. n

Kuikira kumbuyo khalidwe loipa

Wolemba: Rabecca Nsomba

Nthawi zina, amayi amene akukwatiwa amauzidwa kuti asakasiyire wa ntchito kuphika chifukwa wantchitoyo akhoza kulanda banja. Enanso nkumamulangiza kuti asakaleke kudzisamala kuopa akathawidwa.

Tikaonetsetsa palibe vuto ndi kusamala pakhomo, kudzisamalira ndi zina zotero, koma nzolakwika kuika zinthuzi ngati zida zothandizira kuti banja lisathe.

Chifukwa polankhula motere timakhala ngati tikuvomereza kuti zina mwa izi ndi zifukwa zoyenerera popangitsa kuti bambo azichita zibwenzi chifukwa mkazi wake walephera penapake.

Abambo ena amakhala ndi zofooka  zina zikuluzikulu zomwe amayi amazipirira m’makomomu osaganizirakonso kuti mwina apeze mpumulo popeza chibwenzi.

N’chifukwa chiyani zimaoneka zabwinobwino kuti abambo azilephera kupirira nkufika pomasirira Naphiri kuti mpaka apange naye chibwenzi chifukwa waphika bwino?

Abambo otere ngachimasomaso ndipo amakhala kuti Naphiriyo amamusirira kale.

Pali abambo ena autchisi, ena oti akavula nsapato fungo nyumba yonse. Sudzamupeza mayi akuti bola Joni okonza maluwa amadzisamalirako. Mmalo mwake mayi amayesetsa kuti akonze nsapato ndi sokosi za mwamuna wake kuti fungo lichepe.

Koma mzimayi akamveka thukuta, ndiye bambo ali ndi chifukwa chomveka bwino choti akasake chibwenzi? Osamuuza mkazi wako za vuto lake bwa?

Mundimvetse, sindikuti amayi atayirire, koma tizindikire kuti amayi amakhala ndi zofooka. Tsono zofooka za amayi zisakhale zifukwa zokwanira zoti abambo azinka nasaka akazi ena.

Momwe mzimayi amapiririra zofooka za mwamuna wake, mwamunanso apirire za mkazi wake ndipo pamodzi athandizane kukonza zinthu.

Osati mmalo mokonza zinthu tizipititsa patsogolo maganizidwe olakwika omati mayi azipirira pomwe bambo akangoona vuto azikhala ngati wapatsidwa chiphaso chomachita zibwenzi. Izi ndi zolakwika.

Ma ‘playoffs’ afika pena

Wolemba

BOBBY KABANGO

G

anizo lokhala ndi timu ya chi 16 mu ligi ya TNM lakhala loterera pamene nkhondo ya Dedza Young Soccer komanso Super League of Malawi (Sulom) yafika pa lekaleka.

Dedza idatenga chiletso Lachisanu pa 11 March kubwalo lalikulu la milandu mumzinda wa Lilongwe kuletsa kuti Sulom isachititse masewero ofuna kupeza timu ya nambala 16.

Chiletsocho chidaperekedwa ku Sulom Loweruka masewero oyamba pakati pa Airborne Rangers ndi Wizards atachitika kale Lachisanu.

Chiletsocho chidagwira ntchito pa masewero otsatira amene amayenera akhale pakati pa Dedza ndi Airborne Lowerukalo pabwalo la Civo.

Lowerukalo mmawa, Sulom idapita kubwalo kuti akachotse chiletsocho koma mpaka pofika Lachinayi chidali chisadachotsedwe.

Wachiwiri kwa pulezidenti wa Sulom, Daud Suleman, polankhula Lachitatu usiku adati chiletsocho chavuta kuchotsa chifukwa jaji wake adachoka.

“Tidauzidwa kuti jaji wapita ku Zambia, ndiye panopa tikumva kuti jaji wina ndiye athandizire kuti chiletsocho chichoke kuti masewero ofuna kupeza timu ya nambala 16 apitirire,” adatero Suleman.

Timu ya Dedza ikuti ngati Sulom ikufuna kupeza timu ya nambala 16, akuyenera atenge iwo chifukwa ndiwo adathera pa nambala 13 kutsatirana ndi Wizards komanso Airborne.

Koma Suleman akuti njira yosewera ma playoffs ndi yokhayo yomwe Sulom idagwirizana kuti ichitike pofuna kupeza timu imodzi yoonjezera.

Ligiyi tsopano kuyambira chaka chino izikhala ndi matimu 16 osati 15 monga zakhala zikuchitikira koma bungwe la Sulom lidalengeza ganizo lochita ma playoffs patadutsa pafupifupi mwezi chithereni ligiyi.

Ngati chiletsocho chichotsedwe, ndiye kuti Sulom ikuyembekezereka kulengeza tsiku lomwe ma playoffs-wa achitike.

Mwini wake wa Wizards Peter Mponda akuti izi zawasokoneza kwambiri. “Taononga ndalama zambiri, mayendedwe, chakudya komanso malo ogona ndi ndalama zambiri zimenezo,” adatero Mponda.

Wizards ndiyo idapambana m’masewero ake ndi Airborne 2-1.

 

Related Articles

Back to top button