Nkhani

‘Idali nthawi ya mapemphero’

Listen to this article

Mtsikana akadzakulembera SMS yoti ‘I care for you’ ndiye kuti zatheka chifukwa uthengawu ndi waukulu kwambiri. Zidayambanso choncho ndi Alison Banda wa Dziko FM yemwe akukaveka mphete Chifundo Namale pa 30 July 2016.

Awiriwatu akuti akhala akukumana nthawi ya mapemphero ku Calvary Family Church ku Falls mumzinda wa Lilongwe. Inde ndi nthawi ya mapemphero komabe Alison amaponya maso moti pa 30 July kuli kanthu ku Area 36 kulikulu la dziko lino.

Alison ndi Chikondi amangitsa woyera ku Lilongwe
Alison ndi Chikondi amangitsa woyera ku Lilongwe

Mapemphero ali apo, Alison akuti m’mutu mwake mudabwera mawu achikondi kuti akuyenera aponye pa namwaliyu. Zidatheka koma adamukana.

Mphini yobwereza ndiyo imawala, adabweranso ndi nzeru zina koma namwaliyo adapukusabe mutu kukanitsitsa kuti sakufuna zachibwana.

“Mkazi adavuta kuti alole, amaona ngati poti ndine wotchuka sindili siliyasi,” adatero Alison wa m’mudzi mwa Kapindula kwa T/A Kaomba m’boma la Kasungu.

“Ndidayata chikhulupiriro. Kenaka kudabwa wanditumizira uthenga ati wandisowa. Ine chiyani? Kenakanso watumiza uthenga wina ati ‘I care for you.’ Ndidadziwiratu kuti basi ndawina mtima wake,” adatero.

Mosachedwa, akuti adapanga kaulendo kuti akumane ndi namwaliyu, yemwe ndi wa m’mudzi mwa Gonjo kwa T/A Mthiramanja m’boma la Mulanje, ndipo pa 19 February adakumana ndi namwaliyu kuseli kwa NBS Bank mumzindawo ndipo chibwenzi chidayamba.

Chifundo amene ndi mphunzitsi kukoleji ya Exploits University akuti adalola Alison chifukwa cha khalidwe lake.

“Ndinene chiyani ine? Alison ndi munthu wolemekezeka, wokonda, wansangala, ndipo pali zambiri zomwe ndinganene zokhudza mnyamatayu. Pamene ndimati ndimudziwe kaye ndi pamenenso ndimagwera m’chikondi, komanso amakonda Mulungu,” adatero Chifundo.

Shawa ili pa 24 July ku Area 6 ndipo ukwati pa 30 July,  madyerero ali ku Sheaffer Square Gardens mumzinda omwewo. n

Related Articles

Back to top button
Translate »