Nkhani

‘Idali nyengo ya pasaka’

Listen to this article

 

Wina adapitira ntchito yokatola zochitika pa tchuthi chokumbukira mazunzo ndi kuuka kwa Ambuye Yesu pomwe wina adapita kukapuma monga tchuthi koma mapeto ake idasanduka nyengo yoti awiriwa awone zomwe Mulungu adawakonzera.

Mayamiko Seyani, yemwe panthawiyo amagwira ntchito ya utolankhani kukampani ya Nation Publications Limited (NPL) adali kalikiliki kutola zochitika zosiyanasiyana pomwe maso ake adakagwera pa Nicra Chikopa yemwe amadikira abale ake kuti akalowe m’madzi akasambire.

Mayamiko akuti atangomuona Nicra, ntchito yonse idasokonezeka ndipo sadaupeze mtima mpaka adatsatira pomwe padali namwaliyo nkuyamba kucheza naye.

Mayamiko ndi Nicra tsiku la chinkhoswe chawo
Mayamiko ndi Nicra tsiku la chinkhoswe chawo

“Ndidali ndi anzanga pa nthawiyo koma ndidawasiya ndipo nawonso adandimvetsetsa chifukwa sinkadachitira mwina ayi koma kusendera kufupi,” adatero Mayamiko.

Nicra akuti machezedwe a Mayamiko adamusangalatsa kwambiri moti adaiwala zokasambira abale ake omwe amadikira atafika.

“Tidacheza ngati anthu oti tidadziwana kalekale pomwe ayi ndithu kadali koyamba moti adandipatsa chidwi kwambiri,” adatero Nicra.

Chitatha tchuthi, awiriwa akuti adakumananso mumzinda wa Blantyre momwe onse amakhala ndipo macheza awo adapita patsogolo kufikira pomwe Mayamiko adamasuka lilime nkufunsira.

Zonsezi akuti zinkachitika m’chaka cha 2014 ndipo kuyambira apo mpaka lero, chibwenzi chawo chakhala chikuyenda bwino moti pa 4 October chaka chomwe chino adamanga chinkhoswe kuyembekeza ukwati oyera chaka chamawachi.

Mayamiko akuti kwa iye Nicra ndi mkazi yekhayo yemwe adamutenga mtima mpaka njala ya chakudya kutha ndipo akuti salotako zoti nkudzalekana naye.

Nicra naye akuti chake nchisangalalo chokhachokha popeza mwamuna wa kukhosi kwake ndipo naye akuti alibenso nkhawa za tsogolo lowala.

“Palibe yemwe amada nkhawa atapeza chinthu chomwe amalakalaka mmoyo mwake. Ine ndidapeza mwamuna yemwe ndinkalakalaka wachikondi, wachilimbikitso komanso owopa Mulungu,” adatero Nicra.

Mayamiko amachoketra m’mudzi mwa Nankwana kwa T/A Makwangwala m’boma la Ntcheu pomwe Nicra amachokera m’mudzi mwa Nguluwe, T/A Bvumbwe, Thyolo.

Related Articles

Back to top button
Translate »