Nkhani

‘Ife toto takana!’

Listen to this article

Mkozemkoze adanyula maliro aeni. Sinodi ya Livingstonia yatemetsa nkhwangwa pamwala kuti sipepesa monga momwe mafumu ena m’boma la Rumphi alamulira.

Pempho la mafumuwo likudza potsatira chipwirikiti chomwe chidachitika Lachiwiri m’sabatayi poyika m’manda thupi la malemu Chikulamayembe m’bomalo.

Nyondo akulankhula uku mafumu akukambirana zochita

Sinodiyo idakolana ndi mafumu pa maliro a Chikulamayembe pamene idalamula kuti atsogoleri ena monga wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Chilima ndi mtsogoleri wa zipani zotsutsa, Lazarus Chakwera alankhulepo pa malirowo.

Ukali wa mafumuwo udaoneka pamene adakalanda mkuzamawu kuti mlembi wa sinodiyo Levi Nyondo asalankhulenso.

Nyondo sadanjenjemere koma kuwauza mafumuwo kuti ayendetse mwambo wa mapemphero zomwe zidakakamiza mafumuwo kupepesa kuti mwambowo uchitike.

Izi ndizomwe zakwiyitsa mafumuwo motsogozedwa ndi mwana wa Chikulamayembe, Mtima Gondwe yemwe wati sinodiyo idanyazitsa maliro a bambo ake.

“N’chifukwa chake tikupempha kuti sinodi ipepese pa zomwe zidachitikazo. Dziwani kuti adamwalirawo adali bambo anga, ndiye ine komanso akubanja tidakhumudwa nazo,” adatero Gondwe.

Naye gulupu Kawazamawe yemwe amalankhuliranso banja loferedwa adati mafumuwo ali ndi mfundo zitatu.

“Kusalemekeza maliro a mfumu. Kuyambitsa chipwirikiti pamaso pa mtsogoleri wa dziko lino komanso kunena kuti Chilima ndi Chakwera alankhule zomwe zikadayambitsa ndewu,” adatero Kawazamawe.

Koma izi sizikutekesa sinodiyo pamene yati ilibe nthawi yopepesa munthu pa zomwe zidachitikazo.

Mmodzi mwa akuluakulu a mpingowo, mbusa Douglas Chipofya adati boma ndi mafumu ndiwo akuyenera kupepesa mpingo.

“Komanso paja mafumu adapepesa kale kusiwa kuja choncho nkhanizi zidatha basi,” adatero Chipofya.

Mawu a Chipofya adagwirizana ndi mawu a Nyondo amene adatsindika kuti mafumuwo ndi amene akuyenera kupepesa kumpingo.  

Kodi chichitike n’chiyani pamene mpingowo wakana kupepesa? Gondwe adati aona chomwe achite koma sadanene chomwe angachite.

Koma T/A Mwamlowe amene ali pansi pa Chikulamayembe adati pa mwambo wa Atumbuka, mfumu ikalankhula, palibenso amene amalankhula pamwamba pake.

Naye T/A Mwamlowe adati kukadakhala kwabwino mbali zonse zikadadya khonde momwe ndondomeko ya mwambowo ikhalire.

Bungwe lachikhalidwe la Mzimba Heritage Association (Mziha) lidati zikuoneka kuti anthu ena sadapitire kukalira Chikulamayembe.

Mmodzi mwa atsogoleri a Mziha, Ndabazake Thole adati mwambo wakumudzi ulemu umaperekedwa kwa mafumu, ndipo ampingo amabwera n’kumatonthoza anamfedwa.

Naye DC wa boma la Rumphi Fred Movete adati nthawi zonse mfumu ya ndodo ikamwalira, ofesi yake imapanga ndondomeko yakayendetsedwe ka mwambo mogwirizana ndi a banja komanso unduna wa zamaboma ang’ono.

Chikulamayembe yemwe adalongedwa ufumuwo m’chaka cha 1968, adamwalira Lachinayi pa November 29 ndipo adaikidwa m’manda Lachiwiri pa December 4 ku Bolero m’boma la Rumphi. n

Related Articles

Back to top button
Translate »