Nkhani

Imfa ya Chikulamayembe yautsa mapiri pachigwa

Listen to this article

Mkangano wabuka m’banja la a Gondwe pa za munthu yemwe akuyenera kulowa ufumu wa Chikulamayembe.

Mpungwepungwewu wayamba potsatira imfa ya Walter Gondwe, yemwe adali mfumu Chikulamayembe.

Malemu mfumu Chikulamayembe

Mfumu Chikulamayembe idamwalira pa November 29 2018.

Isadamwalire idasankhiratu mwana wake, Mtima Gondwe, kuti ndiye adzalowe ufumu wake ndipo mafumu ena adavomera n’kusainira panganoli ndi Chikulamayembe asadatsikire kulichete.

Koma atamwalira zinthu zidasokonekera kaamba koti mafumu ena akuti Mtima sangalowe ufumu m’malo mwa atate wake kaamba koti ufumuwu si wa banja limodzi, koma umazungulira m’mabanja 12.

Mafumu Achitumbuka akuti kuchokera mu 1795 pamene ufumu wa Chikulamayembe adaukhazikitsa, wazungulira m’mabanja 9.

Mabanjawa ndi a Gonapamuhanya, Kampungu, Pitamkusa, Bwati woyamba ndi wachiwiri, Bamantha, Mkuwayira ndi Mujuma.

Mabanja atatu omwe atsala kuti nawonso alongedwe ufumu wa Chikulamayembe ndi a Mkupa, Mzakwacha ndi Bongololo.

Pachifukwa ichi, mabanja ena akuti ufumuwu sukuyenera kubwerera m’banja la Walter moti akadandaula ku bwalo lalikulu la milandu mu mzinda wa Mzuzu.

Iwo akuti ufumu wa Chitumbuka, umasiyana ndi wa Chingoni, kaamba koti sukhala wa banja limodzi.

Pofuna kumvetsetsa nkhaniyi, Msangulutso udacheza ndi mafumu 6 a m’banja la a Gondwe omwe ndi a Chikalamba, Bongololo, Mkupa, Kalizga, Tawona ndi a Webster omwe atsimikiza kuti adakasumadi ku khoti.

Mneneri wa mafumuwa, Stowel Kalizga Gondwe, adalongosola kuti ufumu wa Chikulamayembe wakhala ukuzungulira m’banja limodzi kuchokera nthawi ya John Hardy Gondwe mu 1977.

Atamwalira John Hardy ufumu sumayenera kupita kwa mwana wake, Walter Gondwe, koma kwa Bwati Gondwe.

“Koma chifukwa choti Walter amakhala bwino ndi anthu, komanso adali wophunzira mafumu adaganiza zomulongabe ufumu,” adatero gogo Chikalamba.

Apa mpomwe padapindika nkhani.

“Padakali pano ife aku banja la a Gondwe tikufuna ufumu wathu uyambenso kuzungulira monga momwe zidaliri mmbuyomu Angoni asadatithire nkhondo.

“Tikufuna dziko lidziwe mwambo wa ufumu wathu, koma anzathu a gulu la Mtima Gondwe sakugwirizana nazo,” adatero Kalizga Gondwe.

Iye adati banja la a Gondwe likuyenera kusankha mfumu kuchokera m’mabanja atatu otsala aja.

“Titakatula madandaulo athu kwa bwanamkubwa wa boma lino, adatibwenza potiuza kuti sagwira ntchito ndi mafumu wamba.

“Pachifukwa ichi tidalemba kalata ku boma yofotokoza madandaulo athu, koma mpaka lero sadatiyankhebe.

“Titaona kuti masiku akudutsa osayankhidwa, m’mwezi wa March tidakasuma ku bwalo la milandu ndipo pakadali pano tikungodikira masiku,” adatero Kalizga Gondwe.

Iye adati asadapite ku khoti, mabanja onse okhudzidwa adakhala pansi ndi mafumu Mwamlowe, Katumbi, woimira anthu pa milandu Victor Gondwe, komanso abizinesi ena monga Alfred Longwe ndi Malopa Gondwe kuti akambirane mwamtendere.

Kalizga adati adagwirizana zoti Mtima apitirize kulamulira, koma akadzangochoka, ufumu udzayambenso kuyenda m’mabanja.

“Koma zomwe zidachititsa kusintha maganizo mpaka poti tikafike ku khoti ndi zoti titachoka kuzokambiranazo, komwe Mtima sadabwereko koma adangotumiza nthumwi,” iye adatero.

M’modzi mwa mafumuwo, Tawona Gondwe, adati zinthu zidalakwika pachiyambi pamene malemu Walter adasankhiratu mwana wake kuti ndiye adzalowe m’malo mwake akadzamwalira.

Polankhulapo imodzi mwa mafumu omwe adawakhazika anthuwa pansi, Mwamlowe idati n’zokhumudwitsa kuti nkhani za ufumu zizipita ku bwalo la milandu.

Iye adati kuzokambiranaku mafumuwa adadandaula za khalidwe la Mtima. “Koma tidagwirizana kuti popeza adasainira kale Walter asadamwalire kuti mwana wakeyu ndiye mlowam’malo, angopitiriza kuti adzayambe kutsatira mwambo wawo Mtima akadzachoka.

“Sindikudziwa kuti chidachitika n’chiyani kuti ayambenso kuwatukwana anzake. Ngati mafumu, tikhalanso pansi kuti tikambirane chifukwa mfumu imayenera izilemekeza anthu ake, izikhala ya bata, komanso yodzichepetsa,” adalongosola Mwamlowe.

Polankhulapo ndi Msangulutso, Mtima Gondwe adati sakudziwa zomwe mafumuwo akukamba.

“Inetu adachita kundiitanita m’chaka cha 2012 kuti ndidzakhale mfumu kuno chifukwa ndinkagwira ntchito ngati community development officer mu unduna woona zoti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo,” adalongosola motero Mtima.

Iye adati ufumu wa Chikulamayembe ndi wake.

Related Articles

Back to top button