Chichewa

Joyce Mhango: Nyale ya zisudzo

Listen to this article

Azisudzo m’Malawi muno akhala akulimbika kutukula lusoli koma chifukwa cha zovuta zina ndi zina mwayi woonekera nkulandira mphotho pa zochita zawo sumapezeka. Ena adayamba kutaya mtima kuti Malawi ingapange zisudzo zoti maiko ena nkutamanda. Izi zili choncho, masiku apitawa, mmodzi mwa ochita zisudzo m’Malawi muno, Joyce Mhango, adalandira chikho cha ulemu pa ochita zisudzo a mmaiko osiyanasiyana a mu Africa. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye pa nkhani yabwinoyi.

Poyamba tafotokoza kuti ndiwe ndani?

Kusonyeza chikho chake: Chavula-Mhango
Kusonyeza chikho chake: Chavula-Mhango

Ndine Joyce Mhango Chavula wochokera ku Rumphi. Ndidasankha kukhala wa zisudzo m’moyo mwanga. Makamaka ndimapanga mafilimu, kuchita zisudzo, kukhala mkonzi wa zisudzo komanso ndimayendetsa kampani ya zisudzo ya Rising Choreos.

Posachedwapa udalandira chikho kukuyamika pa ntchito yako makamaka chifukwa cha filimu yako yotchedwa Lilongwe. Amalawi ambiri ndiwonyadira chifukwa cha nkhaniyo koma sadziwa kuti filimuyi ndiyotani. Ungawafotokozere?

Zoonadi ambiri mwina sakuidziwa bwino filimuyi. Lilongwe ndi filimu yomwe imakamba za mtsikana oyendayenda yemwe ali ndi ana atatu omwe adapatsidwa ndi amuna osiyanasiyana. Iye ali pantchito yabwino koma amapeza ndalama zambiri kuchoka kwa amuna okwatira omwe amagona nawo. Pambuyo pa zaka 7 kale lake la Lilongwe lidayamba kumuweruza ndipo mufilimu yonse samaiwala mawu oti ‘Musandiweruze chifukwa simukudziwa komwe ndachokera.’

Bwanji sitidamveko kuti wakhazikitsa filimi imeneyi m’dziko muno?

Idakhazikitsidwa mu October chaka chatha ku Lilongwe ku Cinema koma anthu ambiri adasemphana nayo. Mapulani okhazikitsanso alipo mu April chaka chino kuti anthu adzayionerere ndipo chimbale chake chifika pamsika posachedwapa.

Udalandira ulemu waukulutu koma ukuona ngati chinsinsi chake chagona pati?

Ndiyambe ndi kunena kuti ndine wodala kukhala mmodzi mwa olandira ulemu umenewu. Ndidapereka filimuyi kwa woyendetsa mwambo kuti ipikisane nawo ndi mafilimu ena ndipo mwa mwayi idasankhidwa kukhala nawo m’gulu la mafilimu omwe adasankhidwa. Ndimakhulupilira kuti kulimba mtima kwanga ndiko kudandithandiza pamphepete pa madalitso a Mulungu.

Zidakutengera nthawi yaitali bwanji kupanga filimuyi ndipo udakumana ndi zokhoma zanji?

Zidatitengera masiku 12 ojambula mosadukiza koma kuti zonse zitheke padatenga nthawi yaitali. Nthawi yovuta kwambiri idali yokonzekera; kusankha anthu oyenera, kusonkhanitsa zofunika ndingoti padalibe kugona. Komabe zonsezo zidapita poti filimuyi yalandirako zikho ziwiri tsopano. Choyamba cha ochita zisudzo mwapamwamba ku Shunaffoz ku Zambia m’chaka cha 2015 ndi ichi chapompanochi.

Related Articles

Back to top button