Nkhani

K10 000 kwa ophunzitsa kumidzi

Listen to this article

Aphunzitsi akumidzi ayembekezere zokoma boma litakwenza ndalama yomwe limawapatsa powalimbikitsa kugwira ntchito kumidzi kuchoka pa K5 000 kufika pa K10 000 pamwezi.

Mkulu wa bungwe la aphunzitsi la Teachers Union of Malawi (TUM), Chauluka Muwake, watsimikiza kuti ndalama yachilimbikitsoyi idakwera kuyambira mwezi wa January chaka chino ndipo aphunzitsi oyenera adayamba kale kulandira.

Muwake wati kukwera kwa ndalamayi kupititsa patsogolo maphunziro msukulu za kumidzi komwe aphunzitsi ambiri amakana kukagwirako ntchito.

“Maphunziro m’sukulu zakumidzi amakhala otsika kwambiri chifukwa chosowa aphunzitsi. Msukulu zambiri kumidzi mumapezeka aphunzitsi ochepa koma ana asukulu ambiri, zomwe zimachititsa kuti mphunzitsi asagwire bwino ntchito yake.

“Koma ndi mmene akwezera ndalama yachilimbikitsomu tili ndi chikhulupiriro kuti aphunzitsi ambiri ayamba kuvomera kukagwira ntchito m’sukulu zakumidzi,” watero Muwake pouza Tamvani.

Ndipo mneneri wa unduna wa maphunziro Rebecca Phwitiko watsimikiza za kukwera kwa ndalama yachilimbikitsoyi ndipo wati ndalama zowonjezerazo zachoka kuthuma la unduna wa zamaphunziro.

“Ndalamayo idakweradi koma sikuti pali ndondomeko ya padera, ayi, chifukwa ndalama zowonjezerazo zikuchoka m’thumba la unduna wa zamaphunziro zomwe aphungu adavomereza mundondomeko ya chuma cha 2013/2014,” watero Phwitiko.

Muwake adadandaulira unduna wa zamaphunziro kuti uziganizira aphunzitsi makamaka pa nkhani ya malipiro ndi kukwezedwa pantchito.

“Nthawi zonse aphunzitsi amakhala m’gulu la anthu olandira malipiro mochedwa komanso pamatenga nthawi kuti ndalama zomwe adagwirira kale ntchito yake (arrears) zituluke. Palinso aphunzitsi ambiri omwe adadutsa kale nthawi yofunika kukwezedwa koma mpakana pano akadali malo amodzimodzi,” adatero Muwake.

Mlembi wamkulu wa unduna wa maphunziro MacPhil Magwira wati undunawu umayesetsa kukonza za aphunzitsi kuti azikhala ndi kugwira bwino ntchito yawo koma umakumana ndi zosokoneza zambiri.

Nduna ya zamaphunziro Lucious Kanyumba wapempha aphunzitsi kuti asamathamangire kunyanyala ntchito yawo pakakhala vuto koma kuti azikumana ndi akuluakulu a kuunduna kuti azigwirizana chochita.

Related Articles

Back to top button