Nkhani

Kainja wadza ndi lumo lakuthwa

Listen to this article

Mkulu wapolisi George Kainja wati adzutsa milandu yonse yogonera n’cholinga chopereka chikhulupiriro mwa Amalawi chokhudza apolisi.

Pocheza ndi wailesi ya Zodiak m’sabatayi, Kainja adati nthawi yoti apolisi ndi anthu azionana ndi diso lofiira yatha kaamba koti afukula milandu yonse ndi cholinga choti chilungamo chioneke.

Kainja: Amalawi alandira chilungamo

Koma akadaulo a ndale ndi ufulu wa anthu adati izi ndi zomwe ambiri amalankhula akangopatsidwa udindo kumene.

Akadaulowa adati Amalawi ayika chikhulupiriro mwa apolisi Kainja akayamba kuonetsa zipatso zake.

Mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera, adasankha Kainja kukhala mkulu wa apolisi kulowa m’malo mwa yemwe amagwirizira mpandowu, Duncan Mwapasa, kutsatira kupuma kwa mkulu wa polisi wakale, Rodney Jose.

“Ndidapanga chisankho chokhala wapolisi mpaka kupuma kwanga. Choncho ndikulonjeza Amalawi kuti nthawi yokhala ndi polisi yomwe amalota akagona yafika tsopano. Ndionetsetsa kuti munthu aliyense alandire chilungamo,” adatero Kainja.

Zina mwa nkhani za mgonagona zomwe Amalawi akhala akuyembekezera chilungamo kwa nthawi yaitali ndi zokhudza imfa ya wophunzira wa ku Polytechnic Robert Chasowa, wogwira ntchito ku bungwe la lolimbana ndi ziphuphu la Anti-Corruption Bureau (ACB) Issa Njauju, kuphedwa kwa Buleya Lule m’manja mwa polisi, komanso kugwiriridwa kwa atsikana ndi amayi kwa Msundwe ku Lilongwe.

Kainja adati nkhanizi azitsatira mpaka Amalawi adziwe zomwe zidachitika, komanso chilungamo chioneke.

Sabata ziwiri zapitazo apolisi adamanga apolisi 13 kuphatikizirapo mkulu wawo wa m’chigawo chapakati, Evalista Chisale, powaganizira kuti akudziwapo kanthu pa imfa ya Lule, komanso adakwizinga akuluakulu awiri a chipani cha UTM powaganizira kuti akukhudzidwa ndi imfa ya Chasowa.

Lule adamangidwa pomuganizira kuti akukhudzidwa ndi imfa ya mnyamata wa zaka 14 wachialubino wa ku Dedza.

Kadaulo wa ufulu wa anthu Charles Kajoloweka adati zomwe adalankhula Kainja n’zothandiza kuti polisi ikhale ya dziko osati ya chipani ngati momwe zinthu zidalili mmbuyomu.

“Chidali chiyembekezo chathu kuti tsiku lina tidzakhala ndi mkulu wa polisi wodziwa ntchito, komanso wokonda dziko lake.

“Timuthandiza kupemphera Kainja kuti ndale zisamumeze ngati momwe zidamezera aakulu ena apolisi m’mbuyomo,” adatero Kajoloweka.Iye adati m’mbuyomu apolisi amatumikira chipani cholamula kuposa dziko zomwe zidachititsa mabungwe kupempha Nyumba ya Malamulo kuti isavomereze Mwapasa kukhala mkulu wa polisi.

Mkulu wa bungwe la Human Rights Defenders Coalition (HRDC), Gift Trapence, adayamikira apolisi pomanga anthu omwe akuganiziridwa kuti adapha Lule.

Iye adapempha apolisi kuti afufuze ndi kumanga anthu omwe akukhudzidwa ndi imfa za Chasowa, Njauju ndi apolisi omwe adagwiririra atsikana ndi amayi kwa Msundwe.

M’mbuyomu otsatira chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) akapalamula milandu samamangidwa, koma chifukwa cha kusintha kwa boma ena ayamba kuimbidwa milandu yosiyanasiyana.

Mkulu wa bungwe la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP), Boniface Chibwana, adati chilungamo mpamene wolakwa ndi wolakwiridwa apatsidwa mpata woti afotokoze mbali zawo, komanso pamene akhutira ndi chilungamo cha woweruza.

“Mmene zidalili m’mbuyomu zikusonyeza kuti wolakwa ndiwo adali ndi ufulu pamene wolakwiridwa adali paululu, komanso adalibe kolowera chifukwa omwe amayenera kuwapatsa chilungamo amapondereza milandu yawo,” adatero mkuluyu.

Kadaulo pa ndale George Phiri adati vuto lalikulu ndi ndondomeko yomwe ilipo yosankhira mkulu wapolisi chifukwa akakhumudwitsa womusankhayo ndiye kuti mchere wake waumapo.

“Chofunika kwambiri n’kusintha ndondomeko yosankhira mkulu wapolisi kuti azikhala woima payekha. Momwe zilili panopa mkulu wapolisi amakhala mkhwapa mwa wolamula n’chifukwa chake malamulo amakomera wolamula okha,” adatero Phiri.

Akadaulowa adagwirizana pa mfundo yoti ndiwokhutira ndi kusankhidwa kwa Kainja, koma adati mpofunika Amalawi apemphere molimbika kuti ndale zisasokoneze.

Iye adati Amalawi adatopa n’kulonjezedwa zinthu zomwe sizichitika n’komwe koma kungogwiritsidwa ntchito kuti ena akwaniritse zofuna zawo pa ndale.

Related Articles

Back to top button
Translate »