Nkhani

Kalembera wafika kummwera

Listen to this article

Kalembera wa mkaundula wachisankho cha chaka cha mawa wafika m’chigawo cha kummwera tsopano ntchitoyi itakumana ndi zokhoma zosiyanasiyana m’maboma a mchigawo chapakati pomwe idayambirira.

Boma la Ntcheu ndi boma lomaliza la mchigawo chapakati komwe kwafika kalemberayu mgawo lachinayi ndipo mgawo lomweli muli maboma a mchigawo cha kummwera monga a Blantyre, Mwanza ndi Chikwawa.

Ntchito ya kalembera

Kalemberayo adayamba Lachinayi ndipo adzatha pa 29 August.

Malingana ndi mkulu woyang’anira zisankho ku Malawi Electoral Commission (MEC), Sam Alfandika, pali chiyembekezo choti pamene ntchitoyi ikupitirira, mavuto omwe amaoneka m’magawo atatu oyambirira achepa kwambiri chifukwa anthu aphunzira mokwanira za kalemberayu.

“Kumayambiriro kuja tidali ndi vuto loti anthu ambiri adali asadadziwitsitse za kalemberayu koma pano ndi mauthenga omwe akhala akuperekedwa, anthu ambiri akudziwa ndipo chiyembekezo n’chachikulu kuti ziyenda bwino,” adatero Alfandika.

Iye adapempha kuti zipani zitengepo mbali yaikulu yomema anthu kuti akalembetse chifukwa anthu omwewo ndiwo mavoti awo.

Mkulu wa bungwe lophunzitsa anthu la National Initiative for Civic Education (Nice) Trust, Ollen Mwalubunju wati bungwelo lipitiriza kuphunzitsa anthu m’madera momwe mukulowera kalemberayu kuti cholinga chenicheni cha demokalase chidzawoneke pachisankho cha chaka chamawa.

“Zimakhala zofoola nkhongono kuona kuti anthu ochepa ndiwo avota kusankha atsogoleri chifukwa zimakhala ngati ena aja angokakamizidwa kutsogoleredwa ndi anthu omwe sadawafune, ndiye tikufuna ulendo uno, aliyense yemwe ndi woyenera kuvota akavote. Chiyambi cha zonse ndi kulembetsa,” adatero Mwalubunju.

Iye adati ndi wokondwa ndi momwe kalembera adayendera m’gawo lachitatu lomwe limachitika ku Lilongwe ndipo adati izi zidatheka chifukwa bungwelo ndi mabungwe ena komanso mipingo ndi zipani adagwirana manja kumema anthu.

Poyamba kalemberayu m’maboma a Kasungu, Salima ndi Dedza, padali mavuto aakulu okhudza kufaifa kwa zipangizo mpakana anthu ambiri sadalembetse. Mavutowa adapitirira mgawo lachiwiri ku Mchinji, Dowa, Ntchisi ndi Nkhotakota moti chipani cha Malawi Congress (MCP) ndi mabungwe ena monga la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) adapempha MEC kuti idzabwereze kalembera mmabomawa.

Mavutowa adadzachepa m’gawo lachitatu lidatha sabata yatha koma padapezeka mavuto ena monga anthu kulandidwa ziphaso komanso miyambo yamakolo yomwe imabwezera kalembera mmbuyo.

Related Articles

Back to top button