Nkhani

Kalikiliki popewa ngozi za madzi

Listen to this article

Pamene nkhani yolosera mvula ili mkamwamkamwa, boma lati lili pakalikiliki kuti madzi osefukira amene amasautsa m’madera ena chaka chino lisakhale vuto la mnanu.

Ambiri mwa anthu omwe amakhudzidwa ndi omwe amakhala m’mphepete mwa madzi makamaka m’maboma a kuchigwa cha Shire: Chikwawa ndi Nsanje. Chaka chatha kusefukira kwa madzi kudankitsa ndipo kudakhudza maboma 18 m’dziko muno, mpaka mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adati dziko lino ndi la ngozi, zimene zidachititsa kuti mabungwe ndi maiko athandizepo.floods1

Malinga ndi mkulu wa nthambi yoona ngozi za dzidzidzi Bernard Sande, chomvetsa chisoni nchakuti ngozi zotere zikachitika boma limaononga ndalama za nkhaninkhani kusamala anthu okhudzidwawo ndi kubwezeretsa zinthu zoonongeka.

Chaka chino chokha boma lidati likufunika K215 biliyoni zoti likonzetsere zinthu zomwe zidaonongeka ndi madzi osefukira dzinja lathali pomwe anthu, ziweto ndi katundu wawo zidakokoloka.

Zambiri mwa zofunika kukonzedwazo ndi milatho, masukulu, misewu, zipatala ndi zogwiritsa ntchito mmalowa zomwe zidaonongeka.

Sande adati chomvetsa chisoni nchakuti anthu omwe amakhudzidwa kawirikawiri amakakamira kukhala kumadzi komwe sikuchedwa kusefukira ndipo adati chaka chino boma likufuna anthu onse okhala mmalo oterewa achokeretu mvula isadayambe.

“Tayamba kale kulangiza anthu kuti achoke m’madera momwe mumasefukira madzi ndipo tionetsetsa kuti onse achoka chifukwa sitikufuna kuti chaka cha mawa tizidzakambanso nkhani yomweyi,” adatero Sande.

Iye adati anthuwa amati sangachoke mmalomo chifukwa makolo awo adamwalira ndi kuikidwa momwemo komanso malo olima ndi kuweterapo ziweto zawo ali momwemo.

Malinga ndi T/A Maseya ya m’boma la Chikwawa, anthu amavuta pankhani yamalo chifukwa amakhulupirira kuti kusiya malo omwe padagona mizimu ya makolo awo kuli ngati kuwagalukira nchifukwa chake safuna kusamuka.

Iye adati vuto lina ndi lakuti malo omwe anthuwo amakhala ndi aakulu kutanthauza kuti atati asuntha ndiye kuti komwe angapiteko malo sangakawakwanire potengera pokhala ndi polima pomwe.

“Kupatula kukhulupirira kukhala pamodzi ndi mizimu ya makolo awo, vuto lina ndi malo okhalapo ndi kulima kumtundako,” adatero Maseya.

Paramount Kyungu ya ku Karonga adagwirizana ndi Sande pankhaniyo ndipo adati palibe phindu kutaya moyo chifukwa chokakamira manda ndi minda mmalo mosuntha kupita kumtunda ndi kudzabwerera mchilimwe.

Related Articles

Back to top button
Translate »