Chichewa

Kalindo walasa!

 

Akulu akale adati kulasa mtengo nchamuna chomwe. Makono tikhoza kunena kuti kuyenda pamsewu utavala ‘mwado’ n’kuvula komwe!

Ndawala ya ‘bunobwamuswe’ yomwe idali mkamwamkamwa sabata zingapo zapitazo m’dziko muno idalephera kuchitika monga momwe ambiri ankaganizira, koma oyendawo adayendabe atabisa kumaso atavala mosadzilemekeza kwenikweni, koma uthenga wawo udafikabe kwa omwe umayenera kupita.

Kuvulatu si chinthu chachilendo, koma kutero pagulu nkumayenda pamsewu thima lili zii ndiye kuti pena pake zaipa.

Pofuna kutsimikizira Amalawi ndi atsogoleri a dziko lino kuti m’dziko muno mwaterera ndi mchitidwwe wachilendo malinga ndi kusowetsedwa ndi kuphwedwa kwa anthu achialubino kwawanda masiku powaganizira kuti ziwalo ndi mafupa awo ndi zizimba zokawira chuma, phungu wa kumwera kwa boma la Mulanje Bon Kalindo, adakonza ndawala yowe adamema anthu kuti ayende ali chinochino mumzinda wa Lilongwe Lachinayi lapitali.

Kalua (kumanzere) kulandira chikalata kwa Kalindo atafika ku Nyumba ya Malamulo
Kalua (kumanzere) kulandira chikalata kwa Kalindo atafika ku Nyumba ya Malamulo

Momwe nthawi imati 8 koloko mmawa, anthu adali atayamba kale kusonkhana pa Roundabout yaku Area 18A pomwe ndawalayo idayambira ulendo wa ku Nyumba ya Malamulo kukapereka chikalata cha kuonetsa kukhumudwa ndi mchitidwewu komanso pofuna kukakamiza boma kuti likhimitse chitetezo kwa maalubino ndi kupereka chilango cha diso-kwa-diso kwa omwe apezeke ndi mlandu wopha anthuwa.

Anthu oyenda pagalimoto zawo ndi m’maminibasi amangoti suzisuzi m’mawindo kuti aone yemwe ayambitse kuvula zovala zake potsegulira ndawalayo koma amadziwiratu kuti sizitheka poona mtsogoleri wa ndawalayo, Kalindo, ali m’kabudula wamkati ndi malaya odula manja, zonse zofiira.

Otsatira ambirinso adavala zofiira ndipo ambiri adali m’makabudula ndi zodula manja kapena kwakwalala kumtunda.

“Ngati woyambitsa wavala choncho ndiye kuti palibepo zovula apa. Mwina agwirizana kuti kuvula kwake kukhale komweku osati mpakana maliseche enieni ngati mmene amanenera,” adatero Innocent Mose, mmodzi mwa anthu omwe adacheza ndi Msangulutso.

Zopatsa chidwi zambiri zidaoneka ndawalayo itayambika pomwe anthu ambiri amakhamukira kumdipitiwo, zomwe anthu ena sadayembekezere polingalira kuti pomwaza uthenga wa ndawalayo amati obwera akuyenera kudzabwera ali psatapsata.

Nyimbo, kuvina ndi kuseka, uku ena atanyamula zikwangwani zolemba mawu osiyanasiyana otanthauza kusakondwa ndi kuphedwa komanso kusowetsedwa kwa maalubino ndizo zidakunga ndawalayo, yomwe idakathera pachipata chachikulu cha Nyumba ya Malamulo komwe oyendawo adapereka chikalata chawo kwa wachiwiri kwa wapampando wa komiti ya zamalamulo m’Nyumbayi, Kamlepo Kalua.

Asadapereke chikalatacho, Billy Mayaya, mmodzi mwa omenyera ufulu wa anthu yemwe adali nawo pandawalayo, adawerenga chikalatacho ndipo atangomaliza padali kuimba ndi kuvina.

Kumayambiriro a sabata yathayi, ndawalayi isadachitike, nduna ya zofalitsa nkhani Patricia Kaliati idanenetsa kuti boma lilibe maganizo obwezeretsa chilango cha kunyonga anthu opezeka ndi mlandu wakupha potengera pangano la maiko onse.

“Dziko la Malawi lidasayina nawo mapangano ambirimbiri okhudza za ufulu wa anthu ndiye sitingabwerere mmbuyo nkuyamba kuphwanya pangano lomwe tidasayina tokha,” adatero Kaliati polankhula ndi atolankhani ku Nyumba ya Malamulo.

Koma mu 2014, dziko la Malawi lidauza msonkhano wa nthambi ya United Nations yoyang’anira za maufulu a anthu ku Geneva, Switzerland kuti boma lilibe maganizo ochotsa chilangochi m’malamulo ake.

Mwa mfundo zina, chikalatacho chidati m’chaka cha 1994, Amalawi adasankha kuti chilango cha diso-kwa-diso chipitirire ngati njira yochepetsera zophana ndiye sangalole kuti aziyendera maganizo a maiko ena.

“Chomwe tikufuna n’chakuti Nyumba ya Malamulo ichotse chiletso choperekera chilangochi kuti anthu onse opezeka ndi ziwalo kapena kupha maalubino komanso milandu ya nkhanza zofanana ndi zimenezi azilangidwa mokwanira,” chidatero chikalatacho.

Zina zomwe amafuna anthuwa n’zakuti apolisi apatsidwe mphamvu ndi zipangizo zokwanira zogwirira ntchito; pazikhala chilungamo pofufuza ndi pogamula nkhani zokhudza maalubino; komanso kuti nkhanizi zizikagamulidwa kubwalo loyenera.

Ndipo ngati kuti adachita kupangana, aphungu a Nyumba ya Malamulo masana a tsikulo (Lachinayi) adadutsitsa Bilu yoti pazikhala chilango chokhwimitsita kwa onse opezeka ndi milandu yopha maalubino komanso kuchotsa chindapusa kwa onse opezeka ndi mafupa kapena ziwalo za anthu.

Mmene Kalindo adanena zoti adzayenda mbulanda pofuna kumenyera nkhondo maalubino, ena ankaganiza kuti ndi zina mwa nthabwala zomwe amachita akavala dzina la ‘Winiko’ wazisudzo, koma Lachinayi adavomereza mwambi uja amati ‘wandisokosa n’kulinga utamva’. n

Related Articles

Back to top button