Chichewa

Kalonga: Waluso lothetsa makhalu

Listen to this article

Kunja kuno oimba ndiye mbwee koma luso lawo limakhala losiyanasiyana. Ena ali ndi mawu anthetemya, ena amaimba zipangiso monga zing’wenyeng’wenye, saxophone, ng’oma pomwe enanso luso lawo ndi kuthyola sitepe. Koma Innocent Kalonga amathetsa anthu mankhalu ndi luso lake-iye amatha kuimba chida chilichonse m’bandi popanda vuto, komanso ndi katswiri pojambula nyimbo. CHIMWEMWE SEFASI adafatsa naye motere:

Amatha kuyimba  chida chilichonse: karonga
Amatha kuyimba chida chilichonse: karonga

Ndikudziwe…

Dzina langa ndine Innocent Kalonga ndimakhala ku Chileka mumzinda wa Blantyre.

 

Kodi Innocent Kalonga amatani pa Malawi pano?

Inetu ndine katswiri wojambula nyimbo zamtundu wina uliwonse kumbali yojambula mawu komanso zithuzi za kanema ndipo ndimapezeka ku Chileka kuno ku Green Arts Studio komwe ndimakhala ndikujambula nyimbo.

 

Zoti uli ndi luso lojambula udazindikira liti?

Ndili ndi zaka 14. Nthawi yatchuthi ndinkakhala ndi chidwi chofuna kudziwa kuti nyimbo amajambula bwanji ndinso kwambiri ndinkakonda kumayesera pakompyuta. Apa mpamene ndidaona kuti zayamba kutheka ndipo padakalipano ndimatha kuimba chida chilichonse chogwiritsidwa ntchito ndi bandi.

 

Kodi luso la zamaimbidwe pa Malawi likupita patsogolo?

Kunena zoona mayimbidwe akupita patsogolo kwambiri moti panopa munthu sungakambe za luso osatchula magulu oimba nyimbo moti masiku ano tikuyenera kuvomereza kuti ku Malawi zoimbaimba zapita ndithu.

 

Ndi magulu ati omwe wajambulirako nyimbo?

Ndajambulako nyimbo za anthu monga Toza Matafale, Wailing Brothers, Limbani Banda ndi anthu ena ambiri, komanso nyimbo zonse zomwe ndidajambula ine palibe anadandaulako.

 

Kupatula kuimba ndi kupeka nyimbo umapangaso chiyani?

Ndimakonda kumvera nyimbo ndipo ndimasangalala kuti takhalapo kalambula bwalo wa oimba amene ndimawakonda.

 

Kodi ndi mavuto ati omwe mumakumana nawo ngati oimba?

Anthu oimba ambiri timasowa thandizo kuti nyimbo zathu zithe kufikira ponseponse. Sitigona poganizira kuti nyimbo tikajambula kuti, adzatithandize kuzifalitsa ndani, nanga tidzagulitsa motani? Timalingaliranso kuti tikonza bwanji ma shows, pompo tikulingalira kuti anthu obwerawo tidzawasangalatsa bwanji?

 

Pali mawu oonjezera?

Ndikuthokoza Amalawi onse chifukwa cha sapoti yomwe amatipatsa komanso NPL pondipatsa mwayi wokhala mlendo sabata ino. n

Related Articles

Back to top button
Translate »