Chichewa

Kamuleni ndi Polisi Palibe

Listen to this article

Tsikulo nkhani idavuta ndi ya anyamata ena aja adabutsa bwalo la milandu m’taunimu. Adaganiza bwanji anthuwa? Uku nkugenda kupolisi wamkulu fodya ali m’thumba la kumbuyo.

“Kukhala mavuto, anthu tsopano aziyenda kuchoka ku Chirimba, Ndirande ndi Chilomoni kupita kuja koonekera ku Chichiri…. Yalakwa,” adatero Abiti Patuma.

Apatu khoswe ali pamkhate koma ndani angaope kuswa mkhate lero? Ndani lero angaloze kuti uwo ndi mkhate? Kuuswa basi!

Tisachedwe ndi anyamata olangika ndi zotsatira za mkalabongo. Nkhani idazunguza anthu pa Wenela ndi ya zochitika ku Polisi Palibe, gulu la masiye.

“Ndikumva kuti nkhani ikuvuta ndi ya kulimbana pankhani ya Kamuleni Kaduwa komanso Udadili Issa omwe anenetsa kuti libolonje lalowa ku Polisi Palibe kuchokera ku Dizilo Petulo Palibe,” adatero Gervazzio, wapamalopo.

“Abodza amenewo. Kodi onsewo ndimayesa adali ndi zipani zawo lero akudzetsa mpungwepungwe kwa Adona Hilida. Kodi Kaduwa suja adazunguza Mpando Wamkulu ndi PDM yake? Nanga uyu Issa sankati tonse ndi Amaravi?” adayankha Abiti Patuma.

Abale anzanga, musandifunse kuti ankatanthauza chiyani chifukwa sindikuuzani. Ndipo mukadziwa mukufuna mutani?

Nthawi yomweyo, Gervazzio adaika nyimbo ya San B komanso Nepman, inde nyimbo imene adaimba uja mnyamata wa ku Chileka.

….Amatigoneka kukada

Amatidzutsa kukacha

Amatidyetsa tikamva njala

Ili ndi pemphero limene lalowerera paliponse pamene kulira ndi njala kwafika pena. Kugona kumsika kuti ugule chimanga, kuotha dzuwa komweko mpaka nthawi ya nkhomaliro opanda chakudya.

Ndimakumbuka tsiku lina titamupanikiza Moya Pete kuti atifotokozere bwino za mmene abweretsere chakudya pano pa Wenela. Mmalo mwake adati: “Amalawi tikutukwanana kwambiri pa Facebook. Tikuphana osati masewera kwambiri.”

“Koma ine ndikuona ngati kuimbanso nyimbo za Michael Jackson kapena Bob Marley nkutaya nthawi. Adaziimba bwino kale,” adatero Gervazzio.

Palibe uyo adayankhira nkhani imeneyo chifukwatu maimbidwe ali m’magulu.

Tili pa Wenela chomwecho adatulukira Fula Kasamba. Tonse chimwemwe chidadzala tsaya. Koma abale, kuphwetsana madzi kotereku bwanji? Walakwanji munthu?

“Ndatulukamo motenthamo. Iwe Tade usandilankhule, sindikufunanso kupalamula. Zoona tsiku ngakhale limodzi osabwera kudzandiona? Ufiti wako udafika pamenepo?” adafunsa Fula.

Abale anzanga, tonse tidangoti chete! Ndikumbuka muja adanenera Chimombo:

M’phirimo m’phirimo m’phiri

Kudzabwera napolo

Napolo lero wabwera. Gwira bango, upita ndi madzi mwaiwe!!!n

 

 

Related Articles

Back to top button
Translate »