Chichewa

Kaneneni akakuchitikirani nkhanza, apolisi auza ana

Listen to this article

Pamene dziko lino limakumbukira masiku 16 othana ndi nkhanza za m’banja, apolisi amema atsikana kuti azikanena akachitidwa nkhanza kwa makolo awo kapena kupolisi.

Mkulu woyang’anira zapolisi ya m’mudzi m’dziko muno, Yunus Lambat, adanena izi pokumbukira maikuwa, amene adayambira pa 25 November mpaka pa 10 December kusukulu ya Blantyre Girls.

Patsikulo, apolisi komanso akuluakulu a makampani osiyana adapita kukapereka uphungu komanso kuthokoza atsikana amene adakhoza bwino m’kalasi.

Tadala: Nkhanza zisatilepheretse

Mtsikana amene adasangalatsa anthu patsikuli ndi Tadala Kadzakalowa wa zaka 11 amene adakhala nambala wani musitandede 8.

Tadala, yemwe akukhumbira atadzagwira ntchito ya udotolo, adaponderera ophunzira 140 m’kalasi mwawo.

Polankhula za tsikuli, Tadala adati iye ndi wokondwa kuti akuluakulu adapeza chabwino kuwafotokozera ufulu wawo komanso zomwe angachite ngati ufulu wawo waphwanyidwa.

“Ndimafuna kudzakhala dotolo, izi sizingatheke ngati wina akupondereza ufulu wanga. Ndadziwa ufulu wanga, komanso zomwe ndingachite ngati wina atandiphwanyira ufuluwo,” adatero iye.

Iye adalangiza atsikana anzake kuti asiye kumwa mowa ponena kuti izi zingasokoneze tsogolo lawo.

Atsikana amene adachita bwino pamaphunziro awo adalandira makope komanso kampani ya Chibuku idawapatsa chakumwa cha maheu. n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »