Chichewa

Kanthu n’khama: Alimi akuchita kuthirira fodya

Listen to this article

Kudula kwa mvula kutionetsa zachilendo mpaka alimi kuchita kuthirira m’minda ya fodya kuti mwina angaphulepo kena kake. Alimi ochenjera akuyesetsa kupulumutsa mbewu zawo pothirira ngakhale kuti ntchitoyi ili yowawa ndi yotenga nthawi. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Lingilirani Chikhwaya, mmodzi mwa alimi omwe akuchita kuthirira fodya kumunda kuti aphulepo kanthu mvula ikapanda kuchita chilungamo.

Ndikudziweni.

Chikhwaya: Zikavute kumsika
Chikhwaya: Zikavute kumsika

Ndine Lingilirani Chikhwaya, mlimi wochokera m’dera la Nkhoma m’boma la Lilongwe.

Mumalima chiyani?

Ndimalima mbewu zosiyanasiyana malingana nkuti masiku ano ntchito ya ulimi njosapanganika. Ukhoza kudalira mbewu imodzi nkugwa nayo osakolola kanthu ndiye potengera upangiri wa alangizi, ndimangobzala mbewu zosiyanasiyana.

Ulimi wanu chaka chino ukuyenda bwanji?

Bambo, kunena zoona zinthu zatembenuka. Tayamba kukhala ndi mantha tsopano kuti kodi chikutilonda nchiyani? Chaka chatha mvula sidalongosoke, anthu sitidakolole bwino ndiye pano pomwe timaona ngati mwina chaka chino tipeza polirira, zikuonekanso ngati mavuto ankira mtsogolo.

Ndiye mwangokhala basi nkumadikira chakudza?

Ayi, tikuyesetsa njira iyi ndi iyo kuti mwina mbewu zina zipulumuke. M’minda ina tili kale bwinoko chifukwa tidatchingira koma m’minda ina monga ya fodya tikuchita kuthirira ndithu ngati ndiwo zamasamba kudimba kuchitira kuti nanga tachoka kale kutali ndipo taononga ndalama, mphamvu ndi nthawi ndiye tikagwere mphwayi pano? Kuli bwino kungodzipereka basi.

Ndiye momwe umakhalira munda wa fodya muja ntchito yake imakhala bwanji?

Tidazolowera. N’kale tidayamba ulimi wa fodya ndipo ululu wake tikuudziwa kale ndipo tidauzolowera. Umatheka kugwira ntchito yakalavulagaga chaka chonse n’kukakhumudwira kokagulitsa ndiye kuli bwino ulimbe nazo zikamadzavuta kumsika ndi nkhani ina.

Ndiye zimakhala bwanji?

Monga ngati ine, munda wanga uli pafupi ndi mtsinje omwe alimi a kuno timagwiritsa ntchito ya mthirira komanso tili ndi sikimu yomwe akatswiri adatiphunzitsa kakololedwe ka madzi ndipo mvula itangoyamba muja tidakololapo madzi. Madzi amenewo ndi omwe tikugwiritsa ntchito pano. Kumunsi kwa mtsinje womwe timadalirawo, tidayamba tautseka kuti madzi asamapite ambiri kupangira kuti mwina mvula ikhoza kutenga nthawi isadayambirenso.

Ndikufuna ndimve za mathiriridwewo potitu munda wa fodya simasewera.

Sitidzipanikiza kwambiri, ayi, timatengako gawo lina lero nkuthirira kenako mawa mbali ina, choncho. Nthawi zina tikakhala ndi nthawi timakathirira mbali ina mmawa madzulonso nkukathirira mbali ina kungofuna kuonetsetsa kuti pomwe mvula izidzabwereranso, fodya adzakhale ali bwino.

Koma muli ndi chiyembekezo chanji pa fodya wanu?

Ngakhale nkhawa ilipo komabe ndikayerekeza ndi momwe zikuonekera m’minda ya anthu ena, mwina fodya wanga akhoza kudzakhala nawo m’gulu la fodya wochititsa kaso chifukwa ngakhale kuli dzuwa chonchi, ayi, masamba ake akuoneka kuti ali ndi mphamvu moti mvula itangoti lero yagwa yambiri, pakhoza kudzuka fodya.

Chaka chatha mvula idachita chimodzimodzi kugwa nyengo yochepa n’kudula kenako n’kudzagobwera moononga. Pemphero lanu n’lotani?

Ayi ndithu, pemphero langa n’loti zinthu zisakhale choncho chaka chino, Mulungu akadatichitira chifundo. Chaka chatha tidaona zowawa kwambiri chifukwa mbewu zambiri zidakokoloka ndi madzi a mvula osefukira moti chaka chino kuli mavuto, makamaka pachakudya, ndiye timati mwina chaka chino tingaoneko chozizwitsa.

Si alimi onsetu omwe akulolera kudzipweteka n’kuthirira, inu alimi omwe akungodikira kumwamba mungawauzenji?

Ayi ndithu, ino si nthawi yomanyanyala zinthu zikapanda kuyenda momwe timayembekezera, koma kuganiza njira zina zokhala mmalo mwa njira yomwe timadalirayo. Mwachitsanzo, pano timayembekezera kuti mvula izigwa mwakathithi kutengera muja idayambira, koma si apa yangodula. Tiyeni tikalowe m’minda basi, tikaoneko kuti tikhoza kupulumutsako chiyani kupangira pamawa. n

Related Articles

Back to top button