Chichewa

Kasambara: Kulimbikitsa anthu mkuimba

Listen to this article

Martha Kasambara ndi woimba nyimbo za uzimu wokhala ku Mzuzu. Iye ali ndi zimbale ziwiri ndipo mu December chaka chino adzakhazikitsa chimbale chake chatsopano chotchedwa ‘Amasamala’. Mtolankhani wathu DAILES BANDA adacheza naye motere:

Tikudziweni….

Ndine Martha Kasambara wa m’mudzi mwa T/A Malanda Ku Chintheche m’boma la Nkhata Bay. Ndili pabanja ndipo ndili ndi mwana mmodzi.

Akutulutsa chimbale chachitatu: Kasambara
Akutulutsa chimbale chachitatu: Kasambara

Mbiri ya maphunziro?

Ndidaphunzira pulaimale yanga pa Lilongwe LEA pomwe ndidalemba mayeso anga a Sitandade 8, sukulu ya sekondale ndidaphunzira ku Chipasula. Ndidakapanga maphunziro a uphunzitsi ku Tanzania komwe ndidaphunzitsa kwa ka nthawi pang’ono ndipo padakalipano ndikupanga bizinesi.

 

Tatifotokozerani mbiri ya maimbidwe anu.

Ndidayamba kuimba ndili wachichepere kwambiri koma chimbale changa choyamba ndidatulutsa mu 2008 ndipo chinkatchedwa kuti Zonse ndi Yesu, chimbale chachiwiri, Nganganga ndi Yesu, chidatuluka mu 2010. Chimbale chatsopano chotchedwa Amasamala ndichikhazikitsa mu December chaka chino.

Uthenga waukulu omwe wanyamula ndi wotani?

Kwakukulu uthenga omwe uli m’chimbalechi ndi wa chilimbikitso kwa Akhristu anzanga m’nyengo zili zonse zomwe iwo akudutsamo.

Yesu amasamala anthu ake ndipo tikamudalira iye sitidzakhumudwa chifukwa chisomo chake ndi chokwanira.

 

Kodi mfundo za nyimbo zimenezi mumazitenga kuti?

Nyimbo zanga kwambiri zimachokera pa maulaliki a kutchalitchi komanso ndikamawerenga Baibulo ngakhalenso nthawi zina zinthu zomwe ndikuona ndi kukumana nazo.

 

Ndi zinthu ziti zomwe mungakonde kuti zisinthe kumbali ya zoimba m’Malawi muno?

M’malo ojambulira nyimbo mwathu mukufunika zipangizo zojambulira nyimbo za mphamvu, ngati mmene kulili ku maiko a anzathu monga ku South Africa, chifukwa nyimbo zimamveka bwino kwambiri.

 

Phindu Mukulipeza mukuimbaku?

Mmbuyomu zinthu zimavuta koma pakali pano ndi chimbale chatsopanoch tsogolo lopindula likuoneka.

 

Pa nthawi yomwe mukungokhala mumakonda kupanga chani?

Ndimakonda kuonelera ma filimu a ku India.n

 

Related Articles

Back to top button