Chichewa

Katsoka: Mtsogoleri wa alakatuli

Listen to this article

 

Ulakatuli ndi limodzi mwa maluso omwe akuphukira kumene m’dziko muno. Zaka zambiri zapitazo, anthu samatenga ndakatulo ngati njira yofalitsira uthenga kapena kuphunzitsa monga momwe zikukhalira pano. Pazaka zochepa zokha, alakatuli m’dziko muno atumphuka ndipo anthu ambiri ayamba kukonda ndakatulo. Alakatuliwa adakhazikitsa bungwe lawo lomwe mtsogoleri wake ndi Felix Njonjonjo Katsoka. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere:

Katsoka ndi mlakatuli wodziwa kuluka mawu
Katsoka ndi mlakatuli wodziwa kuluka mawu

Tandiuza dzina lako ndi komwe umachokera.

Ine ndine Felix Njonjonjo Katsoka. Ndimachokera m’mudzi mwa Ching’amba m’boma la Ntcheu koma pano ndikukhala ku Nkhotakota. Ndidaphunzira za uphunzitsi koma ndimagwira ntchito ya zaumoyo kumbali ya zakudya zamagulu.

 

Utsogoleri wa alakatuli udaulowa liti?

Ndidauyamba m’chaka cha 2009. Malingana ndi malamulo athu, timayenera kukhala ndi zisankho zaka zisanu (5) zilizonse moti panopa tili kalikiriki kuthamangathamanga kuti tipeze ndalama zopangitsira nkhumano ina komwe tidzakhalenso ndi zisankho.

 

Kodi bungwe limeneli lidayamba liti?

Bungweli lidayamba m’chaka cha 1997 pomwe alakatuli adakumana kubwalo la masewero la Kamuzu Stadium. Ena mwa akatakwe omwe adali kumeneko ndi monga Laurent Namarakha, malemu Aubrey Nazombe, Edward Chitseko ndi malemu George Chiingeni. Pa 4 September, 1998, bungweli lidalembetsedwa kunthambi ya kalembera wa mabungwe.

 

Cholinga chake nchiya?

Cholinga cha bungweli ndi kufuna kutukula luso la ulakatuli m’Malawi muno komanso kufuna kufalitsa mauthenga ndi kuphunzitsa anthu kudzera m’ndakatulo monga momwe amachitira azisudzo kapena oyimba.

Kodi munthu amafunika chiyani kuti akhale mlakatuli?

Choyambirira ndi kudzipereka kukhala ndi mtima ofunitsitsa kukhala mlakatuli. Sizilira kupita kusukulu, ayi, ndi luso ndithu lachibadwa. Ine sindidaphunzireko ndakatulo komanso alakatuli ambiri omwe ndimadziwa sadachite maphunziro a ndakatulo, ayi.katsoka

Nanga ndakatulo yabwino imafunika kukhala ndi chiyani?

Ndakatulo yabwino imayenera kukhala ndi phunziro, msangulutso komanso izigwirizana ndi zachikhalidwe kapena nkhani yomwe ikunenedwa. Mundakatulo muli ufulu wosankha mmene ukufunira kuti mavume azimvekera. Palibe malamulo akuti ndakatulo izimveka motere, ayi. Kwathu kuno, ndakatulo zambiri zimakhala zokhudza chikhalidwe cha Chimalawi, makamaka potengera chiphunzitso ndi malangizo.

 

Iweyo udayamba liti ndakatulo?

Ndidayamba ulakatuli m’chaka cha 1994 ndili pasukulu ya sekondale ya Likuni Boys. n

Related Articles

Back to top button