Nkhani

Katundu wobwera ku Malawi ali pachiopsezo ku Mozambique

Listen to this article

Magulu a zachifwamba m’dziko la Mozambique akuchitira mtopola galimoto zonyamula katundu wosiyanasiyana wobwera m’dziko muno kuchokera kumaiko ena podutsa m’dzikolo.

Pali malipoti oti m’dzikomo muli nkhondo yapachiweniweni pakati pa asirikali a boma ndi zigawenga za chipani chotsutsa cha Renamo chomwe mtsogoleri wake ndi Afonso Dhlakama, koma boma la Mozambique lakhala likutsutsa malipotiwo ngakhale anthu ena zikwizikwi athawa m’dzikomo kudzapeza mpumulo m’dziko lino.  Trucks_at_the_border

Mtopolawu udayamba Lachitatu sabata yatha pomwe maguluwo adatentha galimoto ina yomwe idanyamula mafuta a petulo wandalama zokwana pafupifupi K28 378 800 yemwe amabwera m’dziko muno.

Mtopolawu usadaiwalike, maguluwo adatenthanso galimoto zina zitatu Lachisanu masana ndipo ziwiri mwa galimotozo zidanyamulanso mafuta ndipo m’sabata imodzi yokha, galimoto zoyatsidwa zakwana zisanu.

Chiwembuchi chikuchitika kwambiri kwa galimoto zodutsa njira ya Tete ndi Beira ndipo maguluwo sakusankha kochokera kapena kopita galimotozo.

Malingana ndi mkulu wa bungwe la makampani oitanitsa mafuta m’dziko muno, Enwell Kadango, ndalama zokwana pafupifupi K70 miliyoni zapita m’madzi kaamba ka ziwembuzi ndipo iye adati iyi ndi nkhani yoipa pamalonda.

“Mwachidule, galimoto iliyonse yonyamula mafuta, imanyamula mafuta a ndalama zapakati pa K22 miliyoni ndi K23 miliyoni ndiye mukawerengera ndalama zomwe zamwazika nzambiri zedi,” adatero Kadango polankhula ndi Tamvani.

Potsatira zokambirana pakati pa maiko a Malawi ndi Mozambique, dziko la Mozambique lidatumiza asirikali ake kuti azikaperekeza galimoto zotuluka ndi kulowa m’dziko muno podzera m’dzikolo.

Mneneri wa unduna woona za maubale a dziko lino ndi maiko ena, Rejoice Shumba, adatsimikiza nkhaniyi.

Related Articles

Back to top button
Translate »