Chichewa

Khama lipindula paulimi—Phungu

Nthawi zambiri chomwe chimasowa paulimi ndimasomphenya. Alimi ambiri amangolingalira zoti ndikakolola chaka chino ndidzalimanso chaka cha mawa mmalo moti azilingalira kuti chaka chino ndalima ndipo chaka chamawa ndidzakhale pena. Phungu wa kunyumba yamalamulo wa ku mpoto kwa boma la Mangochi Benedicto Nsomba ndichitsanzo chabwino pankhaniyi. Iye adayamba ngati mlimi ochulukitsa mbeu nkusuntha kufika pogulitsa mbeu ndipo pano ali ndi kampani yakeyake yopanga mbeu. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere:

Nsomba: Mbewu zanga nzovomerezeka ndi boma
Nsomba: Mbewu zanga nzovomerezeka ndi boma

Ndikudziweni olemekezeka.

Ine ndine Benedicto Chambo ndipo, monga mwanena kale, ndine phungu wa ku Nyumba ya Malamulo woimira anthu a kumpoto kwa boma la Mangochi. Kunyumba ya Malamuloko ndilinso mukomiti ya zaulimi komanso pandekha ndimalima kwambiri.

 

Inu mulinso ndi kampani yopanga mbewu, kodi mbiri yanu ndi yotani?

Za inetu anthu ambiri sakhulupirira ayi. Ndidayamba zaulimi ngati mlimi wochulukitsa mbewu pansi pa gulu la Association of Smallholder Seed Multipliers Action Group m’chaka cha 2005. Nditachitapo ulimiwu ndidasuntha n’kuyamba kugulitsa mbewu nditatsegula Chambo Agro- Dealers ku Mangochi komweko. Ndagulitsa mbewu mpaka kufika pomwe ndimatsegula kampani yanga yopanga mbewu ya Pindulani Seed Company.

 

Chiyambi chake n’chotani?

M’chaka cha 2010 ndidaona kuperewera kwa mbewu za gulu la nyemba pamsika ndiye ndidaganiza zoyamba kupanga mbeuzi. Ndapangapo mbewu za m’gulu la nyemba kwa zaka ziwiri mpaka kufikira mchaka cha 2013 pomwe ndidaonjezera n’kuyamba kupanganso mbewu ya chimanga kufikira pano.

 

Muli ndi msika wa mbewu zanu?

Kwambiri ndipo mbewu zanga ndi zimodzi mwa mbewu zomwe alimi ambiri akukonda chifukwa zimamera ndi kubereka mwapamwamba kwambiri. Mwinanso ndikuuzeni pano kuti boma lidavomereza mbewu zanga moti pano zili mupologalamu ya zipangizo zotsika mtengo ya sabuside. Apa ndikutanthauza kuti mbewu ina yomwe alimi alime kuchokera musabuside ya m’gulu la nyemba komanso chimanga ndi yopangidwa ndi kampani yanga ya Pindulani.

 

Mumapanga mbewu yochuluka bwanji pachaka?

Poyamba penipeni ndidayamba ndi matani 10 okha ndipo ndimanka ndikukwera pang’onopang’ono mpaka pano ndidakula ndithu. Chaka chino ndapanga matani 340 a mbewu zosiyanasiyana za m’gulu la nyemba ndinso matani 150 a chimanga chamakono chopirira ku ng’amba chomwe boma ndi akatswiri akulimbikitsa. Ndili wokondwa kuti mbewu zonsezi zidatengedwa mupologalamu ya sabuside.

 

Inu mbewu zanu mumazitenga kuti? Si njere iliyonse yomwe ili mbewu.

N’zoona, si njere iliyonse ungabzale n’kumati ndi mbewu. Ine ndili ndi alimi anga ochokera kudera langa omwe ndimagwira nawo ntchito. Ndimawapatsa mbewu kuti achulukitse ndipo ndimawagula pamtengo wabwino ngati njira imodzi yowatukulira. Alimi ambiri panopa kudera kwanga adatukuka moti amangamanga nyumba zamakono za malata kumeneko kuchokera mu ntchito imeneyi.

 

Tinene kuti mudaima pambewu zamitundu iwiriyi basi?

Ayi, ndiye kuti mutu wasiya kuganiza. Lingalirani komwe ndikuchokera kudzafika pano ndiye ndiimire pano? Pakalipano tikuchita kafukufuku wa mbewu za mtedza ndi nyemba zoyenera mthirira zomwe zotsatira zake zikatuluka tikhala tikulimbikitsa alimi kuti azichita ulimi wamthirira wa mbewuzi. Kupatula apo, tikuchitanso katupe wa mbewu zamakono za chinangwa ndi mbatata zamthirira moti ntchito imeneyi yakhala pang’ono kutha kuti tiyambe kugulitsa mbewu yake.

 

Eni makampani opanga ndi kugulitsa mbewu amadandaula za akamberembere omwe amakopera mbewu zawo n’kumaononga mbiri yawo, kaya inu mudakumanapo nazo zotere?

Zimenezo n’zoona, akamberembere alipodi koma chimachititsa kwambiri ndi ogwira ntchito kumakampaniko omwe ali osakhulupirika chifukwa ndiwo amatenga mapaketi n’kumakagulitsa kwa akamberemberewo kuti aziikamo mbewu yachinyengo. Komabe pobwerera kufunso lanu, ife zimenezi sitidakumanepo nazo chifukwa tidapanga njira yoti mapepala a umboni aja amati ‘seal’ oika mkati mwa paketi, timapanga tokha ndiye olo atapeza mapaketi athu, seal ikhoza kuwasowa.

 

Alimi ambiri amakakamira pamodzimodzi zaka n’kumapita, inu mungawauzenji?

Nkhani yaikulu ndi kukhala ndi masomphenya basi. Kumaona patali kuti kodi ineyo lero ndili pano nanga mawa ndidzakhale pati? Mlimi akakhala ndi maganizo otere, zinthu zimayenda chifukwa amayesetsa kuti maloto ake aja akwaniritsidwe, asafere mmalere. China, pamafunika kulimba mtima pochita zinthu chifukwa ukakhala ndi mantha ndiye sizingakuyendere mpang’ono pomwe.

 

Kupatula kuyendetsa kampani ya mbewu, pali china chokhudza ulimi chomwe mumapanga?

Ndili ndi sikimu zingapo ku Mangochi komwe ndimachitirako ulimi wamthirira wa mbewu zosiyanasiyana. Ndidalemba alimi oposa 1 500 n’kuwagawira malo musikimumo kuti azilima. Akakolola, ndimawagula mbewuzo pamtengo wabwino komanso zina zimakhala zawo zakudya pakhomo. Mwezi wa October alimi adakolola nyemba zambiri ndipo ndidawagula zonse pamtengo wa K600 pakilogalamu moti pano ambiri ali ndi ndalama, savutika nyengo yachisangalaloyi.

 

Phindu lina lomwe luntha lanu labweretsa kudera lanu ndi lotani?

Anthu ambiri apeza ntchito monga yosankha, kulongedza, kusanja ndi kunyamula mbewu kufakitale kupititsa m’malo momwe timagulitsira. Amayi ambiri omwe amasowa pogwira, pano akupeza thandizo kufakitale komanso omwewo ndiwo amandigulitsa mbewu ndiye kuti akupha mbalame ziwiri ndi mwala umodzi.n

Related Articles

Back to top button