Chichewa

Khirisimasi ya Niko

 

Nthawi ija yafikanso. Niko adali pa Wenela tsiku limenelo

Abale anzanga, ndikuthokoza Mulungu amene wandilola kuti ndifike tsiku la lero!

Komatu palibe munthu waimva kukoma Khirisimasi kukoma ngati Niko. Mwamuiwala uja ankathandiza gogo uja kuwerenga zaka zambirizo? Mwamuiwala Niko ankakhala kumbuyo kwa gogoyo makamaka tsiku lija adandipeza ndikulima kwathu kwa Kanduku?

Tsonotu sindinena za Tomasi Akwino wanzeru zozana. Sindinganene za Niko yemwetu ngakhale Chichewa chake nchozama zedi.

“Niko, mwaitha. Mwachoka kumpando wosunga zisinsi, mwafika kumpando woulula zinsinsi. Mukamva bwa?” adafunsa Abiti Patuma.

“Mwanaaaa! N’kuuze inetu ndili okondwa zedi. Mukakhala enanu mukadawerenga 1 mpaka 10 koma ine ndikuti penda, penda kuwiri, mwanangu, wansiira kansonjo, njonjonjo, mbiringo, njoli, sansamera, khumi lagwa,” adayankha Niko.

Zinthutu zimasintha. Malisani, Malisani! Zoona Moya Pete nkumutaya Malisani?

“Ndazitaya ndekha. Chilungamo chidaphetsa msemamitondo,” adatero Malisani atafika pamalo paja timakonda.

Gervazzio adaika nyimbo ya Fumbi Jazz Band:

Mmene ntchito yanga yatha

Mwayesa nkhani?

Funani ina nkhani anzanga

Sankhani ina, anzanga!

Palibe icho ndidatola. Kodi si uyu Maliseni adasambwadza Lazalo Chatsika masiku apitawo? Kodi siyemweyu ankanena kuti Moya Pete akukumana ndi anthu ofunika? Kodi si yemweyo zidamutsamwa atanena kuti Moya Pete ali bwino chonsecho atabwera mwini wake adatiuza tonse pa Wenela kuti nyamakazi inamugwira ntchafu?

“Kodi Niko, izi adalankhula Chatsika mukuti nazo bwanji? Nanga enatu akuti akusankhani kuti muchititse nkhani youlula zinsinsi ikhale yovuta, mukutipo bwanji?” adafunsa Abiti Patuma.

William the Conqueror, whose cause was favoured to by Moya Pete, requested quiet clearly stated sequentially created when Thomas Tatertoot took taut twine to tie ten twigs to two tall trees,” adayankha Niko.

Sindidatolepo kanthu. Mwina chifukwa ndidali kulingalira ngati mkazi wanga wokondeka Nambe walandira kuponi.

Gwira bango iwe! Upita ndi madzi a Khirisimasi ndi Nyuwere. n

Related Articles

Back to top button