Chichewa

Koma pa Wenela zidzatheka?

Listen to this article

Tsikulo tidakhala pa Wenela. Tidali kusowa cholankhula. Kodi ndi January ameneyu?
Ayi ndithu. Kukazinga chimanga chisanachoke m’munda.
Nyimbo zomwe ankaika Gervazzio tsikulo palibe icho ndinkatolapo. Mvula idali ikugwa.
Wamkana ku Europe! Wamkana ku America! Wamkana mwana wake!
Iyinso nyimbo idali kuphulika pomwe tidamva kuti ndege zidali kutera pa Wenela. Pajatu pa Wenela pali bwalo la ndege.
Tidangomva mkokomo wa ndege.
Timayesa ikutera.
Inkatera.
Koma siyidali ndege.
Lidali lichero.
Tonse tidathawa!
Licherolo mudali Joloji Chadyaka yemwe ena amayembekezera kuti afikira ku Lumbadzi. Koma abale anzanga, ngati kuli munthu amene ndimadabwa naye, ndiye ndi ameneyu.
Nanga inu, munthu anganene za kutsitsa mpweya n’kumatsika lichero pa Wenela mungadabwe nazo?
Komatu nkokomo umene unkamveka pa Wenela aliyense adathawa.
Tsono. Tsono. Tsono.
Sindinadabwe ndi za Chadyaka. Chadyaka ndi Chadyaka basi kaya munena za mmera, kaya soya, kaya nsetanyani, kaya thonje. Chadyaka ndi chadyaka basi!
Ndimamukumbuka mkulu ameneyu.
Adayenera kufika ku ukwati wa mwana wa mnzanga 2 koloko. Mwambowo umayenera kutha 4 koloko. Iye adafika 4:20pm.
Inetu zonena zambiri ndilibe.
Ndiye mwati anthu otchuka atatu anabwera pa Wenela nthawi imodzi? Mwati uyu Dona adatenga Melise ndi Davide anafika pa dambwe lathu ku Kumbali wafika m’dziko muno kudzatenga ana ena? Bwanji osatenga nkhalamba ya chibwana Joloji Chadyaka? Bwanji osatenga Moya Pete?
Ndiye mwati kwafikanso uyu Rihhhhon?
Pakadakhala kuti Abiti Patuma alipo nkadamufunsa, koma anali atapita kofufuza nkhanizo. Pa Wenela panalibepo.
Gwira bango, upita ndi madzi! n

Related Articles

Back to top button