Nkhani

Konzani mavuto a kayidi, litero khoti

Listen to this article

Khoti la First Grade Magistrate m’boma la Dowa, lalangiza boma kuti likonze  ena mwa mavuto omwe akayidi akukumana nawo m’ndende za m’dziko muno.

Mavutowa ndi monga kuthinana kosayenera m’zipinda zogona, kuchepa kwa chakudya, komanso kuchedwa kutumiza kwawo akayidi ochokera maiko ena omwe atsiriza kugwira chilango chawo m’dziko muno.prison

M’kalata yomwe alembera boma kudzera kubungwe lake loyang’anira ndende m’dziko muno la Prison Inspectorate Committee, bwaloli lati akaidi omwe ali m’ndende za m’dziko muno akuvutika kwambiri maka kaamba kakusalabadira kwa akuluakulu woyang’anira ndendezi.

Mneneri wa boma yemwenso ndi nduna yofalitsa nkhani Jappie Mhango, akana kutsirira ndemanga pankhaniyo. Iwo akankhira kwa nduna ya za chilungamo Samuel Tembenu. Omwe nawonso akana kuti nkhaniyo sikukhudza unduna wawo koma wa za m’dziko, komwe kuli Jean Kalirani.

Koma Kalilani, sitidathe kuyankhula nawo,  kaamba kakuti panthawi yomwe timalemba nkhaniyo nkuti iwo ali kunja kwa dziko lino.

Kalatayo yomwe idalembedwa pa 28 August, 2015, ndipo amene adasayina ndi majisitileti Amurani Phiri, imodzi mwanjira yodalilika yochepetsera mavutowa ndi kulimbikitsa chilango chogwirira kuchokera kunyumba kwa akayidi omwe apalamula milandu yochepa. Bwaloli lati pakali pano ndende ya Maula mumzinda wa Lilongwe, ndi yomwe yanyanya kukhala ndi akayidi ambiri zedi.

“Ndidakayendera ndende ya maula pa 27/08/2015, patsikuli ndidakapeza akaidi 2 532. Kuphatikizapo akaidi ochokera kunja kwa dziko lino okwana 569, omwe mwa iwowa, 230 ndi nzika za dziko la Ethiopia.

“Ndipo ambiri adali atatsiriza kale kugwira ukayidi wawo, koma ankadikira kuti boma lipeze ndalama zowatumizira kwawo. Ndipo pankhani ya chakudya, ndendeyo imagwiritsa ntchito  matumba 32, a ufa wa mgaiwa kudzanso matumba 8 kapena 9 a nyemba patsiku,” adatero iye.

Mneneri wa Malawi Prison Service (MPS) Smart Maliro, pambali polonjeza kwa masiku angapo kuti atero, sadayankhe mafunso omwe tidamutumizira.

Ndipo poyankhapo pa nkhaniyo, mneneli wa ku nthambi yoona za anthu olowa  ndi kutuka m’dziko, Joseph Chauwa,  wati nzoonadi kuti mwezi wa August chaka chatha, kundendeyo kudali nzika za maiko ena, maka za ku Ethiopia zokwana 400.

Koma Chauwa  adati ndi thandizo la ndalama zochokera ku bungwe la International Organization for Migration (IOM), nzikazo zidatumizidwa kwawo ndi matikiti a ndege omwe bungwelo lidagula, nzikazo zidapita kwawo.

Related Articles

Back to top button