Chichewa

Ku Machinga akonzekera ulimi wa fodya

Listen to this article

 

Alimi a m’makalabu 7 ati chaka chino akonzeka kulima fodya wochuluka ncholinga chosintha mabanja awo pachuma popeza iwo amakhulupirira kuti fodya ndi mbewu yomwe imabweretsa chuma chochuluka pakhomo.

Nkhaniyi idadziwika pamene Kampani ya Japanese Tobacco International (JTI) sabata yatha idapereka feteleza pangongole kwa alimi ochokera m’dera la mfumu Ngokwe m’boma la Machinga pamwambo womwe udachitikira pamsika wa Ngokwe ndipo alimiwo adatsindika kudzipereka paulimiwu chaka chino kuti Malawi asimbe lokoma ndi ndalama zakunja zomwe zimathandizira kuyendetsa ntchito za chitukuko m’dziko.

Tobacco_hanger

JTI idaganiza zochita machawi pofuna kuwagwira mkono alimiwo kuti akwaniritse masomphenya awo.

Kampaniyo idakongoza alimiwo matumba a feteleza okulitsa a Super D Compound kwa onse omwe adapanga makalabu a zaulimi kuti iwo alime fodya wochuluka ndi kumusamala bwino.

Mmodzi mwa alimiwo, Sitola Banda, adati JTI ikuthandiza alimi a m’bomalo kukwaniritsa malingaliro awo kuti chaka chamawa boma lipeze fodya wochuluka.

“Talandira ngongole ya matumba a feteleza wokulitsa ndipo tikukhulupirira kuti tigwiritsa ntchito thandizoli moyenera. Makalabu omwe ndi aakuluakulu adakongozedwa feteleza matumba 200 pofuna kuti achilimike ndi ntchito za kuminda yawo. Si bwino mlimi kusiya ntchito za kumunda n’kumapita uku ndi uku koyang’ana feteleza m’nyengo yoti ulimi wafika kale pampondachimera,” Banda adatero.

Iye adati dera la Ngokwe makedzana lidali ndi minda ya fodya yochuluka ndipo alimi ankatumiza fodya wambiri kumisika ya fodya m’dziko muno. Choncho iye adapempha alimiwo kuti adzipereke kotheratu kaamba koti nalonso boma limaika chidwi pafodya kuti chuma chiyende bwino.

“Tiyeni titukule dziko lathu potenga nawo mbali paulimiwu. Mlimi wochenjera adafesa kale fodya wake kunazare ndipo pakadalipano maso ali tcheru kuyembekeza kumwamba kuti mvula igwa liti,” adaonjezera Banda.

Mlimiyu, yemwe amachokera m’kalabu ya Kondwerani m’mudzi mwa Muwawa, T/A Ngokwe, adathokoza kampani ya JTI kaamba kowapatsa poyambira, zomwe zakhazikitsa pansi mitima ya alimi m’deralo.

“Tikuthokoza JTI popereka ngongole yochuluka chotere, apatu sitijejemajejema mvula ikayamba kugwa. Talandira matumba a feteleza okulitsa motengera muyezo wa fodya yemwe tidasayinirana kudzagulitsa kukampaniyo ndipo tikuyembekezanso kulandira matumba ena a feteleza wobereketsa posachedwapa,” adatero Banda.

“Tingopempha Chauta kutipatsa mvula yokwanira chaka chino kuti tikwaniritse khumbo lathu potukula mabanja ndi dziko lathu. Tikuyamikiranso kampaniyi popeza ikutilimbikitsa kubzala mitengo yambiri m’malo momwe tadulamo mitengo yogwiritsira ntchito paulimiwu kuti tichepetse kuononga chilengedwe kuderali,” adaonjezera motero Banda.

Palinso mabungwe ena monga Mardef, omwe akuthandiza alimi kuderalo powapatsa ngongole ya zipangizo za ulimi kuti asasowe pogwira pamene ntchito ya kumunda yayambika. makedzana lidali ndi minda ya fodya yochuluka ndipo alimi ankatumiza fodya wambiri kumisika ya fodya m’dziko muno. Choncho iye adapempha alimiwo kuti adzipereke kotheratu kaamba koti nalonso boma limaika chidwi pafodya kuti chuma chiyende bwino .“Tiyeni titukule dziko lathu potenga nawo mbali paulimiwu,” adaonjezera Banda.

Mlimiyu, yemwe amachokera m’kalabu ya Kondwerani m’mudzi mwa Muwawa, T/A Ngokwe, adathokoza kampani ya JTI kaamba kowapatsa poyambira, zomwe zakhazikitsa pansi mitima ya alimi m’deralo.

“Tikuthokoza JTI popereka ngongole yochuluka chotere, apatu sitijejemajejema mvula ikayamba kugwa. Talandira matumba a feteleza okulitsa motengera muyezo wa fodya yemwe tidasayinirana kudzagulitsa kukampaniyo ndipo tikuyembekezanso kulandira matumba ena a feteleza wobereketsa posachedwapa,” adatero Banda.

“Tingopempha Chauta kutipatsa mvula yokwanira chaka chino kuti tikwaniritse khumbo lathu potukula mabanja ndi dziko lathu,” adaonjezera motero Banda.n

Related Articles

Back to top button