Chichewa

Ku Nkhoma sakugona ndi mthirira

Listen to this article

Amati mmera mpoyamba. Ukalephera kukonzekera koyambirira ntchito yonse imayenda mwapendapenda mpaka zipatso zake zimakhala zokhumudwitsa. Ino ndi nyengo ya dzinja ndipo ulimi wagundika ndi wamvula, koma alimi ochangamuka pano ayamba kale kukonzekera za mthirira wachilimwe chomwe chikubwera kutsogoloku. Ena mwa alimi omwe akuonetsa chitsanzo chabwino pakukonzekera mthirira wamtsogolo ndi a ku Nkhoma m’boma la Lilongwe. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi wapampando wa gulu la alimiwa, Lingilirani Chikhwaya pazomwe akuchita, motere:

Chikhwaya: Sitivutika kumbali ya chakudya
Chikhwaya: Sitivutika kumbali ya chakudya

Ndikudziweni wawa…

Ine ndine Lingilirani Chikhwaya ndipo ndine wapampando wa alimi a mthirira omwe amathandizidwa ndi bungwe la Vision Fund Malawi kudzera m’thumba la ngongole za ulimi la Mthirira Loans.

 

Mulipo alimi angati?

Tonse tilipo alimi 222 omwe timathandizidwa ndi Vision Fund Malawi koma aliyense ali ndi munda wakewake momwe amalima mbewu yomwe iye akuona kuti imuchitira bwino ndipo apindula nayo.

 

Ndi mbewu zanji zomwe zimalimidwa kwambiri?

Ambiri amalima chimanga, nyemba, tomato, anyezi ndi ndiwo zamasamba zosiyanasiyana. Ambiri mwa ife timakonda kasakaniza monga kubzala chimanga limodzi ndi nyemba kapena kugawa kuti mbali ina tomato, ina anyezi ndipo ina masamba monga chomoliya, mpiru kapena kabichi.

 

Ulimi umenewu ukukupindulirani bwanji?

Ulimiwu tikupindula nawo kwambiri chifukwa usadabwere, ambirife tinkavutika kwambiri kupeza zipangizo zaulimi dzinja likafika kusowa pogwira, koma pano zinthu zidasintha. Tikamachita mthirira wathu timakhala tikusunga pang’onopang’ono ndalama mwinanso nkumaguliratu zipangizo zaulimi n’kumasunga. Tikatero, dzinja ngati lino likafika timakhala tilibe nkhawa. Kupatula apo, sitivutika kumbali ya chakudya chifukwa timati tikamadya zamvula, zamthirira zikucha kuti zamvulazo zikamadzatha, tidzayambe kudya zamthirira.

 

Mukuoneka kuti muli kalikiriki m’munda wa mthirira pomwe lino ndi dzinja simukupotoza pamenepa?

Ayi ndithu, umu ndimo timachitira. Kuteroku tayambiratu kukonzekera mthirira wachilimwe chikubwerachi. Pali zambiri zomwe timayenera kupangiratu monga kusunga madzi okwanira, kuteteza maiwe anthu kuti asadzadze komanso kutchingira m’malo momwe mumathamanga madzi kuti asaononge nthaka. Kungolekerera nthaka imakokoloka ndiye poti munthu udzayambe kulima ulimi wamthirira zofuna zimachuluka monga kusonkhanitsa manyowa obwezeretsera nthaka yomwe idakokolokayo.

 

Panopa yakula ndi ntchito iti?

Monga ndanena kale, pakalipano ntchito yaikulu ndi yosunga madzi. Ulimi wathu wamthirira timadalira msinje ndiye chaka ndi chaka ngati panopa timatchingira kuti madzi asathawe. Timapanganso mizere ikuluikulu yotchinga madzi kuti azilowa pansi kuti mvula ikadzatha, pansi padzakhale chinyezi kwathawi yaitali tisadayambe kuthirira.

 

Tafotokozankoni nkhani ya misika, mumagulitsa kuti zokolola zanu?

Ambiri mwa ife timadalira kugulitsa kumisika ndi kupikulitsa kwa anthu omwe amakagulitsa kumsika. Si misika yodalirika, ayi, komabe timapezamo kangachepe. Pakalipano omwe amatithandiza ndi ndalama za ngongole a Vision Fund Malawi akutithandiza kuyang’ana misika yodalirika moti posachedwapa tikhala tikusimba lokoma.

 

Mudalingalirako zopanga magulu ogulitsira katundu wanu pamodzi?

Maganizo amenewo ndiwo tikupanga tsopano nchifukwa chake tili kalikiriki kusakasaka misika yokhazikika komanso paja ndati pakalipano mlimi aliyense ali ndi ufulu wolima mbewu yakukhosi kwake ndiye tikufuna kuti tikapeza msika wokhazikika, tizidziwa mbewu zoyenera kulima. Nanga si msika wapezeka kale?

 

Kaya tsogolo la ulimi wanu mukuliona bwanji?

Tsogolo ndi lowala kwabasi chifukwa momwe tidayambira ndi pomwe tili pano zikusiyana kwambiri. Mbewu zomwe tinkakolola kale ndi zomwe timakolola pano zimasiyana kwambiri chifukwa pano tidapatsidwa upangiri wapamwamba ndi alangizi odziwa ntchito yawo. Chiyembekezo chathu nchakuti m’zaka zikudzazi tizidzalima ndi kukolola mbeu zoti mwinanso nkumadyetsa chiwerengero cha anthu ochuluka chifukwa, mwachitsanzo, chaka chino tathandiza anthu ambiri ndi chimanga chomwe tidalima kusikimu ndipo nafenso tapeza phindu lochuluka kwambiri.

 

Malangizo anu ndi otani kwa alimi anzanu?

Malangizo anga ndi oti alimi asamakonde kukhala pansi ayi. Ntchito yathuyi imasiyana kwambiri ndi ntchito zina chifukwa ife ndiye timadyetsa mtundu wonse. Tizionetsetsa kuti mvula ikamapita kumapeto, ntchito ya kusikimu yayamba ndipo chilimwe chikamapita kumapeto, tizionetsetsa kuti tayambiratu kukonzekera ulimi wa mthirira wotsatirawo ngati momwe tikuchitira ifemu. Izi tikuchita apazi ndi chiyambi chabwino chifukwa sitidzakhala ndi ntchito yambiri mthirira ukamadzayamba.

 

Kutanthauza kuti panopa kusikimu kuzingokhala?

Zimatengera mlimi kuti pologalamu yako njotani. Paja pali mbewu zina zomwe zimafunika kubzala mwakasinthasintha monga nyemba ndi chimanga ndiye ngati mlimi akukonzekera kudzabzala chimanga chamthirira, akhoza kubzala nyemba kapena mtedza musikimu kuti akamadzakolola, adzaponyemo chimanga. Nkhani nkukonzekera bwninobwino kumayambiriro kwake. n

Related Articles

Back to top button
Translate »