Nkhani

Ku Nsanje akukana zosamuka

Listen to this article

“Ife zosamuka ayi,” yanenetsa gulupu Karonga ya kwa mfumu yaikulu Mlolo m’boma la Nsanje.

Mawu a mfumuyo akudza pamene anthu 56 pofika Lachinayi sabata ino adatsimikizika kuti amwalira ndi mvula yosalekeza yomwe idazunguza dziko lino sabata yatha.

Malinga ndi nthambi yoona za ngozi zogwa mwa dzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (Dodma), nyumba 184 589 omwe ndi anthu 922 945 akhudzidwa. 

Lachitatu Dodma idachenjeza anthu amene akukhala malo angozi kuti asamukire kumtunda chifukwa a zanyengo alosera kuti mvulayo itha kubweranso.

Komabe izi sizikusuntha gulupu Karonga amene wati anthu aiwale zosamukazo chifukwa pali zambiri zomwe ataye ngati atasamuka.

“Lero ndine mfumu, kuti ndisamuke kupita dera lina ndiye kuti ndikakhala munthu wamba, mukupaona bwanji pamenepo,” adatero Karonga, kulankhula mmalo mwa mafumu ake ang’onong’ono.

Mfumuyo limodzi ndi anthu ake atsakamira pachilumba cha Makhanga. Ndi pakati pa madzi, sangapite madera ena pokhapokha akwere bwato lomwe ulendo umodzi ndi K5 000.

Mfumuyo yatinso anthuwo atha kusamuka ngati atawapezera dera lomwe kulibe anthu kuti aliyense akakhale ndi udindo wake komanso malo okwanira.

Koma mlembi wamkulu wa Dodma Wilson Moleni adati apita ku Nsanje kukawapemphabe anthuwo kuti asamuke.

“Akuti mvulayi ibweranso, kutanthauza kuti zinthu zifike polakwika kuposa apa, ndi bwino kusamukira malo okwera kuti tipewe,” adatero Moleni.

Ngozi ya mvulayi yakhudza maboma 14 m’dziko muno koma boma lomwe lakhudzidwa kwambiri ndi Chikwawa chifukwa anthu 8 ndi amene afa.

Mu 2015 dziko lino lidakhudzidwanso ndi ngozi ya madzi yomwe idadza chifukwa cha mvula yosaleka. Anthu 79 adafa ndi 153 adasowa. Anthu 638 000 adakhudzidwa. n

Related Articles

Back to top button