Chichewa

Kubzala mtedza mwa makono

Listen to this article

Akatswiri a zakafukufuku wa mbewu m’dziko muno adafufuza njira ya makono yobzalira mtedza imene ili ndi kuthekera kochulukitsa zokolola za mbewuyi pamalo ochepa. Njirayi imadziwika kuti double row planting m’Chingerezi. Mlangizi wa mbewu m’boma la Thyolo Aggrey Chiwala adafotokoza zambiri za njirayi. ESMIE KOMWA adacheza naye motere:

Kodi njira ya makono yobzalira mtedza ndi iti?

Mlimi amadzichulukitsira zokolola akatsatira njirayi

Chidule chake timangoti ndi njira imene timabzala mtedza wathu m’timizere tonse tiwiri timene timalemberera pamzere umodzi wa mbewuyi.

Izi zimathandiza kuti pamzere umodzi umene kale timangobzalapo kamodzi basi tsopano tizitha kubzalapo kawiri.

Nanga ubwino wa njirayi ndi wotani?

Ubwino wake ndi woti mlimi amakolola zochuluka pamalo ochepa chifukwa amakhala wachulukitsa mbewu pamzere umodzi.

Malingana ndi a zakafukufuku, njirayi imachulukitsa zokolola kuposa theka ndi ndalama za mlimi ndi magawo opitirira 60 pa 100 aliwonse.

Ubwino wina ndi woti mlimi savutika ndi kupalira chifukwa mtedza umaphimba bwino pamwamba osasiya mpata choncho udzu umakanika kukula kaamba ka kusowekera dzuwa lokwanira.

Kodi mbewuzi siziphangirana zofunikira kuti zichite bwino?

Ayi, chifukwa zimatalikirana pa mlingo woyenera.

Izi n’chifukwa mzere timautambalalitsa ndipo mmalo mobzala pakati timabzala m’mbali choncho zimatayana.

Nanga mizere yake mlimi amayenera aikonze motani?

Mizere imayenera ikonzedwe motalikirana ndi masentimita 75 ngati mmene imakhalira ya mbewu monga chimanga ndipo kutalikitsa mopyola apa ndi kungoonongapo malo.

Mizereyi isalazidwe pamwamba kuti pakule ndi masentimita 50.

Izi zimathandiza kuti mlimi akwanitse kulemberera pamwamba pa mzerewo timizere tobzalamo mbewu tokwana tiwiri.

Timizere tobzalamoti timayenera titalikirane ndi masentimita a pakati pa 25 ndi 30.

Kodi mabzalidwe ake amakhala otani?

Mlimi amayenera abzale m’timizere tiwiri tonse ndipo mapando pa kamzere kamodzi azitalikirana ndi masentimita a pakati pa 10 ndi 15.

Izi zikuyenera kuchitikanso pa kamzere kenako kufikira mlimi amalize kubzala munda wonse.

Pa phando lililonse abzalepo mbewu imodzi ndipo kuya kwake kukhale masentimita apakati pa 5 ndi 8.

Nanga chimachitika n’chiyani mlimi akabzala pamwamba kapena akazamitsa kwambiri?

Mlimi akabzala pamwamba mbewu zina zikhoza osamera ngati mvula yachedwa kubwera chifukwa dothi la pamwamba silichedwa kuuma.

Akabzala mozamitsa zimachedwa kumera kapena kukanika kutuluka kumene.

Kodi pa hekitali mlimi kuti abzale njira yotereyi akufunika mbewu yochuluka bwanji?

Kuchuluka kwa mbewu pa hekitala kumasiyana malingana ndi mbewu. Pali mbewu zina zimakhala zazikulu choncho zimalemera kwambiri pamene zina ndizazing’ono zopepuka.

Chifukwa cha ichi kuchuluka kwa mbewu pa kilogalamu iliyonse kumakhala kosiyana.

Ichi n’chifukwa chake kuchuluka kwa mbewu pa hekitala kumakhala pakati pa makilogalamu 80 ndi 100.

Nanga mlimi akabzala amayenera asamalire motani kuti mbewuyi ichite bwino?

Chachikulu ndi kupalira kuti m’munda musamakhale tchire.

Poyambirira mlimi akhoza kugwiritsa ntchito khasu koma mbewuzo zikakula ndi kuyamba kutulutsa tizingwe timene timazika pansi ndi kubala mtedza azingodzula udzu ndi manja.

Izi zimathandiza kuti asasokoneze mtedzawo chifukwa kupanda kutero, zokolola zimatsika ndithu.

Kodi kuipira kwa njirayi n’kotani?

Njirayi imafuna mbewu yochuluka pafupifupi kawiri kusiyana ndi kubzala kamodzi pa mzere.

Ntchito nayo pobzala imachuluka choncho pamafunika aganyu ochulukirapo kuti itheke.

Nanga malangizo anu omaliza ndi otani?

Ngati mlimi akufuna apindule pogwiritsa ntchito njirayi asanyozere kubzala ndi mvula yoyamba malingana ndi nthawi imene mvula imayambira kudera lake.

Akuyenera kusankha mbewu yabwino ndi kubzala pamalo a dothi losakanikirana.

Related Articles

Back to top button
Translate »