Chichewa

Kucheza ndi Ibu Mphanje: Gaba wochemerera Bullets

Listen to this article

Anthu otsata masewero a mpira wa miyendo alipo ambiri koma ena amaonjeza kukonda kwake. Ena adachita kufika popereka maina achilendo kumatimu omwe amachemerera ati pofuna kuwopseza anzawo. Ibu Mpanje ndi mmodzi mwa ochemerera timu ya Big Bullets yomwe eni ake amati ‘Timu ya Fuko’ kapena ‘Ma Palestina’. Ndidacheza naye motere:

Mphanje: Masapota tionjezera mphamvu
Mphanje: Masapota tionjezera mphamvu

Moni wawa komanso ndikudziweni?

Ine ndine Ibu Mpanje kwathu n’ku Nathenje koma ndikukhala m’tauni ya Lilongwe. Ndimakonda kwambiri masewero a mpira wa miyendo moti timu yanga ndi Big Bullets. Anthu ambiri amandidziwa ndi dzina lakuti Gabadinho, osati osewera mpira uja, ayi, koma wochemerera.

Tsono dzina la Gabadinho lidabwera bwanji?

Basi kumpira anthu ambiri amandipatsa ulemu pa nkhani yochemerera ndiye nthawi ija kudadzatulukira Gabadinho wa mpira ija anthu amatengera momwe adagwedezera iye nkumandiitana ndi dzina lomwelo.

Anthu ambiritu amakonda kudzitcha okha maina a anthu otchuka, sizili choncho ndi iwe?

Ayi, nokhaso mudaona momwe zidalili kuja kokhala anthu ochemerera momwe ndidagwedezera  ochemerera matimu ena omwe samafunira Bullets zabwino. Zimakhala mommuja nthawi zonse kukakhala mpira, makamaka wa Big Bullets, timu yanga kuyambira kalekale.

Umangokonda mpira basi kapena uli ndi mbiri iliyonse pamasewerowa?

Mpira ndinkasewera kalekale kuyambira kupulayimale mpaka m’makalabu ena ndi ena moti kusiya ndidasiyira pa timu ya KIA. Ndasewerako malo osiyanasiyana m’galaundi koma malo omwe ndidasewera kwambiri ndi kutsogolo. Kuvulala ndiko kudandichititsa kuti ndisiye kusewera mpira. Ndidavulala kamodzi ndiye kuyambira pomwepo ndinkati ndikasewera mpira ndimadzutsa vutolo.

Malingaliro ako adali otani panthawiyo?

Panthawiyo ndinkafunitsitsa kudzasewera m’matimu akuluakulu makamaka ya Big Bullets  moti sindikaika kuti chipanda kuvulalako, n’kadafika pomwe ndimafunapo. Anthu omwe adandionererako nthawi imeneyo akhoza kufotokoza bwino za luso lomwe ndidali nalo moti pano ndimadandaula kwambiri chifukwa ndidasiya mpira ndisadasewereko mutimu ya Flames.

Chifundo chosechi pa timu ya Bullets bwanji supikisana nawo pamaudindo kuti uzitumikira nawo?

Ayi, zinthu zimafunika kupatsana mpata. Ngati pali ena omwe aonetsa kale mtima wofuna kutumikira, ena mumafunika kuthandiza amenewo kuti pakhale umodzi chifukwa nonse mukamalimbirana, mkangano suchedwa kuyamba, ayi.

Sabata yathayi mwasewera masewero awiri omwe simudapambaneko. Zikutanthauzanji kwa iwe ngati wochemerera?

Poti awo adali masewero ongopimana mphamvu ndiye sindingazitengere kwenikweni, koma tikudikira ligi ikayamba ndiye anthu adzaone Bullets yeniyeni. Mudaona nokha ligi yathayo momwe Bullets idavutira, chaka chino tiposa pamenepo ndipo ifenso ochemerera tionjezera mphamvu kuti anyamata osewera nawo adzadzipereke kotheratu.

 

Related Articles

Back to top button
Translate »